Abu faruq sheikh Abdurazaq chitemwe

Abu faruq sheikh Abdurazaq chitemwe

Share

Mulibe ubwino mu foni yomwe siyikuitanira ku umodzi wa Allah (Tauheed) ndi kulimbana ndi zinthu zopeka Bidia mu Deen ya Allah subhahanahu wataala.

01/05/2026
28/04/2026

UFULU NDI MPHAMVU MU CHISILAMU

ASALAM ALAIKUM WARAHMATULLAH WABARAKATUHU AZICHIMWENE NDI AZICHEMWALI MU DEEN

Chisilamu chinalamula kuti munthu ayenera kumvera konse Kwa makolo ake ndipo izi Allah analumikiza ndi ibaadah yake ndipo Kuchitira zabwino makolo ndi ibaada pambuyo popembedza iye.
((وقضى ربك الا تعبدوا إلا إياه وبالوالدين احسنا))
Ndipo walamula mogemula m'mbuye wako Allah kuti usapembedze China chilichonse koma Iye yekha ndipo makolo ako awiri uwachitire zabwino.

Koma ngakhale zili chonchi pali zinthu zomwe chisilamu chinapeleka Ufulu ndi mphamvu kuti wina aliyense azichitire yekha motsatira Malamulo a chisilamu ndipo kuteroko sikuwerengedwa Kuti kunyoza Kapena kusalabadira makolo.

1.KUSANKHA BWENZI LAKO LOTI UKHALE NALO PA BANJA (NIKAH)

pambuyo poti chisilamu chatikakamiza kumvera komanso kulemekeza makolo chisilamu sichinsmkakamize Munthu kuti makolo ake ndi omwe amusankhire kapena kumkakamiza Kuti atenge bwenzi limene iwo alikonda Mu njira ina iliyonse kuti akhale mamuna /mkazi wako omanga naye banja pokhapokha zitagwirinana ndikufuna komanso kukonda kwako, Koma ngati siudafune komanso siudakonde uli ndi Ufulu komanso mphamvu zowakanira kuti izi sindikupanga nawo ndipo kutero sikusanduka kuti wanyoza Kapena kusawachitira zabwino ayi.

Izizitu chimodzi modzi ngati banja unalisiya ndipo ukufuna kubwelera iwo alibe Ufulu okuletsa kuti iyeyo osamubwelera Koma Kwatiraniii wina ayi. Ulengizi wawo tiumva ngati kholo lako Koma chisankho cha ukwati chili ndi iwe mwini wako.

Kumbali ya mtsikana timamva Kuti bambo ndi yemwe amufunire mwana wake mamuna okwatirana naye inde izi zili choncho ndithu koma ziyendera kukonda kwake ndikusangalatsidwa ndi mamunayo ndipo ngati sanamukonde ali ndi Ufulu owuza bambo wake kuti Adadi uyu ayi ndisakireni wina.

Dziwani kuti ngati kholo likakamiza mwana pa Za ukwati kwa bwenzi lomwe sakulifuna Kapena kumuletsa Za bwenzi lomwe mwana akufuna ngati lili la chisilamu komanso khalidwe la bwino kholo lotere limawerengedwa Kuti ndi la nkhanza kwa Ana ake choncho liyenera kulangizidwa mwa Ubwino pa mchitidwe otsutsana ndi Sunnah wu.

2.CHUMA CHAKO

Chisilamu chikulamula kuti ife tithandize makolo athu ndipo ichi ndi chikakamizo ndithu ndipo ngati siungatero Dziwa Kuti ukupanga uchimo mmachimo akuluakulu ukuyenera toba yokwanira pa mchitidwe onyansawu. Koma ngakhale zili choncho sizikutanthauza kuti kholo lako ndilo liziyendetse chuma chako Kapena kutenga mopanda chilolezo chako ayi, kapena kutenga chuma cha mwana wina ndikukampatsa mwana wina kapena kutenga ndikukaonjezera pa chuma chawo pokhapokha ngati pali kusaukira pa chumacho ndipo iwe siukwapatsa potengera Hadith yomwe Mtumiki sallallahu alayhi wasallam adati
وأنت ومالك لأبيك
Iweyo ndi chuma chako ndi za abambo ako.

Koma kuyankhula uku sikuti kukupeleka mphamvu Kwa kholo pa chuma chako ayi.

MALANGIZO OPITA KWA MAKOLO NONSE ACHISILAMU

Eee Inu makolo athu okondedwa muopeni Allah pa Ana anu imeneyi ndi Aamanah yomwe Allah wakusungitsani choncho onetsetsani kuti zofunikira kukuchitirani Anawo akukuchitirani Koma Zomwe sizili mu Ufulu ndi mphamvu zanu zisiyeni. Kholo la bwino kwambiri ndi lomwe lili loleza mtima pa Ana ndipo limapewa mawu obweretsa tsoka pa Ana ake, khalani achifundo komanso okhululuka kwambiri pa Ana anu khalani olimbikira maduwa abwino kwa Ana anu komanso kukhala nawo pa mavuto ndi pa mtendere mwa chikondi chanu cha nthawi zonse.

Oh Allah akhululukireni komanso achitireni chifundo makolo athu ngati momwe amkachitira ife tili ang'ono.
Oh Allah kwa amene makolo onse kapena m'modzi adamwalira chonde Allah walitsani manda awo apangeni kukhala otakasuka ndipo tsiku la Qiyaamah Allah mukatikumanitse ndi iwo mu jannatul firdous Allahummah Aameen ya Rabbali Alameena.

SubhanaAllah wabihamudihi subhanaka Allahummah wabihamudika Ash hadu allailaha illa anta asitaghafiruka wa Aatubu ilaika.

24/04/2026

UTHENGA WA CHILIMBIKITSO KU ANTHU TAPHUNZIRA MAKA MAPHUNZIRO A DEEN YATHU YA CHISILAMU

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته
AZICHIMWENE NDI AZICHEMWALI MU DEEN
قال رسول الله صلى الله عليه وسلم :خيركم من تعلم القرآن وعلمه
Mtumiki sallallahu alayhi wasallam adati :wabwino mwa inu ndi yemwe mwaphunzira Quran ndi kuiphunzitsa.

Ndikukumbukira ndili ku primary school Ku Mangochi lslamic center mu 2006 - 2009 ndinali ndi mzanga Abdullah sayfullah chumi yemwenso anali classmate wanga Komaso timapanga Za karate limodzi.

Titamaliza mu 2009 wina aliyense analowera kosiyana Ine ndinalowera Ku Balaka islamic lnstitute komwe ndinakapangira secondary school Yanga Koma nzangayu sindikudziwa kuti analowera kuti nevertheless, tinakumana mu 2017 pa m'baluku omweo tinasowa ndipo chaka chino ndinafufuza nambala yake Alhamudulillah ndinaipeza.

Ndayamba kumufusa nzanga uli Kuti komanso ukupanga zotani for daily living?
Nzanga anandiyankha mochititsa khaso Komaso momvetsa chidwi amvekere mzanga ine ndili kwathu ku Mozambique ndipo ndikupanga izi :

(A)Ndimalima ndi cholinga choti ndizidya osati business ayi
(B) Ndimaphunzitsa Tawuheed m'mudzi mwakwathu omwe unali pa Bidia nthawi yaitali ndipo palibe chomwe ndimapeza komanso iwowo palibe chomwe amalandira Kuchokera kwa amwenye Kapena aliyense kupatula Maphunziro basi 😭😭😭😭😭misonzi idatsika m'maso mwanga yozidandaulira Kuti Lero alipo anthu omwe akupanga Dawah mitima yawo ili yoyera yofunitsitsa malipiro ochokera Kwa Allah basi yaa Allah.

Phunziro lanji lomwe tapeza apa?

Ndikunenayu ndi mnyamata wa zaka zathu amene akufunika Umoyo wa enjoy ndi banja lake, azitchena mikanjo yabwino azidya zabwino and Mkazi wake azitchena koma wallahi limodzi ndi kuthekera konse ndi mapepala oti akhoza kukaonetsa Ku ma bungwe Kapena kampani ali nawo koma kapolo wa Allah Sheikh Abdullah sayfullah chumi wasankha kukhala Umoyo otere kamba kofuna ku wachotsa anthu mu mdima wa bidia ndikuwayika mukuwara ndi dangalira la Tawuheed wallah Allah amutsegulire makomo ama riziq komanso ampatse Moyo wa utali kuti ummah upindule Allahummah Aameen.

Funso kwa inu ndi ine kodi tikutani ndi Maphunziro athu omwe tili nawo? Tikukhala moyo wabwino magetsi alipo, ma foni abwino, tikutchena mikanjo ya bwino, ma banja athu ndi abwino wosangalala, mwezi ukatha tikuyembekeza kulandila kena kake, tikupanga chani ndi Tawuheed?

Fone zathu zikugwira ntchito yanji pa Deen
Eee inu ma huffaz omwe mwaloweza Quran mukutani ndi Quran pa maso pa Allah?
Eee inu amene mwasoma zitabu zikugwira ntchito yanji zitabu pa maso pa Allah?

Nthawi yanu itati yafika lero tikayankha chani Za Maphunziro athu?

Tiyeni tiphunzire ndikuphunzitsa Tawuheed ma sheikh nthawi yathu ndi yomweyi, tisaiwale izi Mtumiki sallallahu alayhi wasallam adati :
من كتم علما علمه الجم يوم القيامة بلجام من النار
Yemwe wabisa Maphunziro omwe waphunzira akalowetsedwa chigwe cha moto mphuno mwake ndikumakokedwa ngati bulu m'moto.
KOMANSO adati :
لن تزال قدما عبد يوم القيامة حتي يسأل عن اربع وذكر منها وعن علمه ماذا عمل به.................... الي آخر
Silikasuntha phazi la kapolo tsiku la Qiyaamah mpaka atakafusidwa za zinthu zinayi ndipo adatchula m'menemo Za Maphunziro ake kuti unagwiritsa ntchito yanji............

Allah subhahanahu wataala atichitire chifundo tonse komanso atiteteze ndikutiongolera ku njira yake yoongoka kufikira imfa zathu Allahummah Aameen.
SubhanaAllah wabihamudihi subhanaka Allahummah wabihamudika Ash hadu allailaha illa anta asitaghafiruka wa Aatubu ilaika.

23/04/2026

_KAMVEDWE KOLAKWIKA KUMBALI YA MA SHEIKH NDI ZOKHUZA MA CHIMO

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته
Azichimwene ndi
azichemwali anga Mu Deen.

KODI MTUMIKI NDI NDANI?
Mtumiki ndi munthu ochokera mu ana Adam anavumbulutsidwa mawu kuchoka Kwa Allah kuti awauze anthu, koma iwo anali otetezedwa ku Machimo ndi zolakwika kotero sikunapezeke kuchimwa Komaso kulakwitsa pa iwo.
(2)KODI MASHAABAH NDI NDANI.

Ndi anthu omwe anamuona Mtumiki ndi kumukhulupirira ndikumwalira ali Asilamu. Iwo anali okhululukidwa ku Machimo kotero kulakwika komwe kudachitika pakati pawo kunali kokhululukidwa. Kotero ife ngati ahlu Sunnah wal jamaah tiyenera kukhala chete pa Chilichonse chomwe chidachitika pakati pa mashabah.

(3)KODI SHEIKH NDI NDANI

Ndi munthu kuchokera mu ana Adam adapatsidwa uzindikiri wa Deen ndi mwini wake Allah subhahanahu wataala. Koma sali otetezedwa ku Machimo salinso otchingiridwa Ku zolakwika Ndi Nsambi kotero kwa iwo kuchimwa sichinthu chachilendo Koma akulowa mu kuyankhula kwa Mtumiki sallallahu alayhi wasallam koti :
كل بني آدم خطاء وخير الخطائين التوابون
Mwana wina aliyense wa Adam ndi ochimwa ndipo wabwino mwa ochimwa ndi yemwe amati akachimwa amapanga toba.

Pali anthu omwe amakhala ndi maganizo olakwika kwa ma sheikh mu zinthu izi
1/KUCHIMWA KWA SHEIKH
Anthu ambiri amati ngati sheikh wapanga chimo Kwa iwo umakhala Umboni kumanso mangolomera oti nawo azichimwa ati poti sheikh wa chimwa Dziwani kuti inu mukafusidwa zanu ndikuyankha nokha ndipo sheikh akafusidwanso zake.
2/PAMENE SHEIKH WACHITA TCHIMO
Anthu ambiri akamva Kapena kuona sheikh wachita tchimo amapezano zochita komanso zofalitsa ndikupezeramo mwayi pozimitsa noor ya Allah kudzera kuchimwa kwa sheikh. Dziwani mchitidwe uwu ndi oipa komanso onunkha sheikh ndi munthu ndipo akhoza kuchimwa ngati munthu ndiipo kupulumuka kumachimo si kamba koti wa soma Koma ndi Taufiq ya Allah choncho wina aliyense yemwe wachimwa Tiyeni timuchitire maduwa kuti Allah amukhululukire komanso amupatse hidaya osati kumuyalutsa ndikumuika poyera Kuti Dziko lidziwe ayi. Mtumiki sallallahu alayhi wasallam adati من ستر مسلما ستره الله يوم القيامة
Yemwe wamubisila msilamu choipa ndi choyaluka chake Allah azamubisila choipa ndi choyaluka chake tsiku la Qiyaamah.
NOTE :
TCHIMO LA LIKULU LOMWE LIMAONONGA NTCHITO ZA MUNTHU
Tchimo lomwe limaononga ntchito za munthu ndiye الشرك kuphatikiza Allah ndi zinthu zina koma Machimo onse saononga ntchito za munthu koma kuti umangofananiza mulingo wanu wa zabwino ndi zoipa ndipo tsiku la Qiyaamah zonse zikayikidwa pa sikelo ndipo komwe kukalemereko ndikomwe udzapite, zikakalemera zabwino ukapita ku jannah ndipo zikakalemera zoipa ukapita Ku moto والعياذ بالله العظيم
Choncho msilamu wa bwino ndi yemwe amapewa Machimo pokana kasakaniza ndipo amachulukitsa kupempha chikhululuko Kuti zabwino zichuluke.

Allah subhahanahu wataala atichitire chifundo tonse komanso atiteteze ndikutiongolera ku njira yake yoongoka kufikira imfa zathu Allahummah Aameen.
SubhanaAllah wabihamudihi subhanaka Allahummah wabihamudika Ash hadu allailaha illa anta asitaghafiruka wa Aatubu ilaika.

Abu faruq sheikh Abdurazaq chitemwe swalihiyyu
Mafunso ndi mayankho online classes
#0693909242
WhatsApp group

20/04/2026


Tawuheed lslamic TV channel

25/03/2026

Asalam alaikum warahmatullah wabarakatuhu brothers and sisters mu Deen ya Allah subhahanahu wataala :

Ndafusidwa funso lonena kuti malamulo akutinji pa mkazi yemwe akuletsa mamuna wake kukwatira mitala?

Kuyankha kunali choncho :

Mitala adaloleza ndi Allah Tabaraka wa Ta'ala yemwe adalenga Chilichonse, Mwini wa chilichonse ndipo Allah ngati waloleza chinthu palibenso Yemwe angaletse mpaka tsiku la Qiyaamah.

Ngati anadzudzulidwa yemwe ndi wabwino ku zolengedwa zonse za Allah kamba konena uchi sindidzadyanso mpaka Allah kutsitsa Ayah kuti:

يا أيها النبي لم تحرم ما أحل الله لك تبتغي مرضات ازواجك والله غفور رحيم.
Eee iwe Mtumiki chifukwa chani ukuletsa zinthu zomwe Allah waloleza.............?

Ngati uyu ndi Mtumiki yemwe wahy umatsika Kwa iye zili bwanji munthu yemwe ngakhale maloto a jannah sanalotepo akaletse Mamuna kukwatira mitala?

1.Ndikufuna ndilankhule nanu sister kuti muopeni Allah Yemwe analoleza Ndiye muziike pa scale kuti ineyo ndine ndani kuti ndikazipange Haram Zinthu zomwe Allah anazipanga Halaal?

2.Ndimafuna ndikukumbutseni Kuti banja ndi ma Riziq ochokera kwa Allah omwe amampatsa yemwe wamufuna Choncho ngati kuli kuopa kuti mwina mamuna wanga akakwatira mitala tisauka yedzamirani Kwa Allah Yemwe amagawa ma riziq.

Iwe Mzibambo yemwe ukusiya kukwatira mitala kamba koti mkazi wako wakuletsa unayenera kumuopa Allah Tabaraka wataala yemwe wakuloleza mitala osati kapolo olengedwa ndi yemwe wakuloleza.

Chimene ine ndingalangize ndi chakuti ukwatire mitala kamba koopa Allah ndipo usakwatire mitala kamba koopa Allah osati kamba ka munthu olengedwa ndi Allah.

Allah subhahanahu wataala atichitire chifundo tonse komanso atiteteze ndikutiongolera ku njira yake yoongoka kufikira imfa zathu Allahummah Aameen.
SubhanaAllah wabihamudihi subhanaka Allahummah wabihamudika Ash, hadu allailaha illa anta asitaghafiruka wa Aatubu ilaika.

Want your school to be the top-listed School/college in Vereeniging?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Website

Address


Abu Hurairah Crest 2
Vereeniging