12/01/2026
🌹 FAVOUR 🌹
💔NO PLACE IN MY HEALING ❤️
WRITTEN BY NISHER PART 7
0735681767.
"Dzuro kuchipatala doctor akuti mimba yanga ili mu fallopian tube ikukulira momwemo ndiye mwana sakula ndipite akaichotse kapena kuipopa , mwana ndinamupeza movutika uja ine."
Hope analira.
"Ayi sizoona osati mwana wanga Hope ."
"Ndikuuza ndimasowa Kuti ndilankhula bwanji , dzuro usiku sindinagone Nelson chikundiona ndi chani ? Akundilodza ine abale Favour."
"Ndani ?"
"Babe ukukumbukila ndinakuuza zakuti bola banja lathu lizapeze ntendele ."
"Eya ."
"Zotsatila zake ndi izi mwana akuvuta nyumba Muno ukuganiza ngati ndi za norm ."
Nelson anakhala chete osayankha chilichonse Hope akupukuta nsonzi mbali Ina akusisimisa mtima.
"Hope wati doctor ananena Kuti chani?"
"Nelson sindingamabweleze zikundiwawa kwambiri." Mwana wankazi anaimilira kupita kukalowa kuchipinda.
Nelson anakhala chete Kaye amazinvela chisoni, anali atagula kale njinga ya mwana anapita kukagwira kenako anakhala pansi ndikugwira Mutu.
Analowa kuchipinda kupeza Hope akulira, Koma anthu ena kkkk ali ndi ma plan.
"Hope basi tonthola mulungu akalora azatipasatso mwana."
"Mtima wanga ukuwawa Nelson."
"Zimachitika , tonthola mawa tipita tonse kuchipatala pokakupopa osadandaura nkazi wanga ndili nawe nthawi zonse."
Hope anadzuka kumusamilisa Nelson Mutu wake pachifuwa.
______________
Luca anakhala osalankhula ndi munthu nyumba muja.
"Kodi Lu lero wakhumudwa ndi chani kkkkk ?" Kunali kufunsa Kwa ntsikana amane amakonda kumakacheza Ku room yomwe Luca ndi anzake amakhala.
"Kaya mwina waiwala mpeni mimba mwa patient kuchipatala."
"Ahahaha ." Anthu aja anayamba kuseka Koma Luca ndi Francisco anangokhala chete poti madziwa chilungamo.
[Kenako Francisco anangoimilira ndikupita panja.
Anthu Aja ataona Kuti Luca sakuseka anakhala chete kumamuyang'ana modabwa .
Macheza sanapitililenso.
Tsiku lotsatira.
Kunja kutacha Luca anapita pa bed pomwe Francisco anagona ndikumugwededza.
"Hey hey tadzuka."
"Bwanji amwene udakali m'mawa."
"Pepa , Koma ndikupita Ku ntchito ndiye ukatsala sizokumana ndi ujayo komaso paja ndanena kuti nambara uchotse."
"Oky."
Lucas ananyamuka ndikumapita. Kenako Francisco anaomba nsonyo ndikulowa bulangeti.
Masana atakwana Francisco anamuimbila phone Favour.
"Ngriii!"
"Hello!"
"Ulibwanji? Bwanji sukundiuza chili chonse."
"Mmm Lucas wavuta Favour."
"Ndiye wagonja, mm oky chabwino."
"Wait favour ndifunse, umandikonda?"
"Kwambiri France ngakhale sindikukudziwa bwino."
"Ineso ndimakukonda ndipo osandikaikila."
"Nanga bwanji ukulora ena kapena ndinene Kuti bwanji ukupeleka mwayi wako kwawina."
"Ndinakudziwa chifukwa cha iyeyo sindikufuna upeze vuto."
"Ndibwera madzuro komweko Lucas akaweruka ndilankhule naye ndekha, asandipangile zochita kudziwana sichifukwa."
"Calm down."
"Osadandaura." Favour anadula call.
Amaoneka Kuti wakhumudwa kwambiri.
__________________
Hope ndi mamuna wake anatengana kupita Ku banja kutsogolo akuti akachotse mimba mu tubu.
Atafika Nelson anakhala panja ndipo Hope analowa nkati.
"Mulibwanji sister ndikuthandizeni bwanji ?"
"Doct ndikupatsan ndalama Koma ndikufuna zochepa mukamu signise mamuna wanga Ngati ndikuzachotsa mimba , Koma ineyo mimba ndilibe, ndikupatsani ndalama."
"Ooh oky poti ndindalama."
"Eya sindikufuna banja langa lithe." Doctor uja nayeso ii kaitana kavula nthawi yomweyo anatenga ma pepala kukamupatsa Nelson.
"Signani apa bambo?"
"Mumasainaso?" Nelson anafunsa.
"Eya." Kenako Mwana wamamuna anasaina ndipo kenako doctor anabwelera nkati , anamuuza Hope Kuti akakhale kwina kwake mpakana nthawi yomwe amuuze, ndipo anapanga zomwezo.
Mosadya nthawi, nthawi yomwe amafuna inakwana kenako hope anatuluka ngati akudwala.
"Zatheka Bea ?" Nelson anafunsa.
"Eya Koma kuwawa eish ndiye anandipatsa mapilis awa."
"Osadandaura ukhala bwino."
Anthu aja anapita kukakwera galimoto ulendo wakunyumba..
Atafika Nelson anakamusiya Hope nyumba iye anapita kwa mai ake kukawafotokozela chilichonse.
"Mmm zoona Koma Nelson mtima wanga wapweteka."
"Osadandaura Amai zimachitika."
"Ofunika kumupemphelera molimbika."
"Iyeso akuganiza Ngati ndi favour Koma anthu andiuza Kuti sanalozedwe zimachitika , Koma ndipemphela ."
"Zoonadi mwana wanga. Ndikamuona akadzuka poti wanena Kuti wagona."
"Okay."
Nelson anatuluka panja.
_______________
Madzuro Favour anapita Kwa Luca's.
"Gogogo."
"Eya lowani ." Munthu anayankha nkati ndipo Favour analowa.
Anthu onse anamulonjela.
"Kodi umanena zoona Kuti ubwela eti?"
"Lucas anamufunsa Favour.
"Eya ndimakufuna kwambiri ndiye poti Pali anthu tilankhulane panja.
"Oky ."
Anthu Aja sanachedwe anatuluka.
"Lucas ndakupeza nkhani yake ndiya Francisco, ukudziwa ine ndi iwe palibe chilichonse ndipo Francisco ndi mamuna amene ndikufuna please musiye andikond."
"Amakonda akazi sangakuthanditheze."
"Ali dele nkulinga utayenda naye, ndisiye zione ndekha."
"Iyeyo ndi oyipa pokuonekelesa ndimati akudziwe Monga anzanga kenako akukapangaso izi behind my back , anthu okuti aziwa town chifukwa cha ine, achina ndiolose ndikakudyele kutali."
",iwe ndi brother wanga."
"Ayi osazandiitanaso brother."
"Oky Koma ndapempha ndanena ndisiye Ine ndi Francisco l love that guy."
"Not under my watch."
"Ndikumangisa ndilibe nazo ntchito olo tidane walowa nkati."
Lucas sanayankhe.
Favour mukhumudwa anachoka ndikuwatsanzika anthu Panja kenako ananyamuka kumapita atakwiisana ndi Lucas.
"Ndafulumila kumupanga force nkazi uja ndimafunika kudekha aziwe Kuti Franc ndioyipa, oky ndiona Kuti ndi ndaitani." Anazilankhulira okha bambo Lucas.
_____________
Hope anadzuka apongoz Ake anapita kukamuona ndikupemphela naye kenako anakhala kumacheza , Koma anamuletsa kugwira ntchito akuti akudwala.
____________________
Tsiku lotsatira.
Lucas sanapite kuchipatala anali pakhomo.
Kenako anamuitana Francisco.
"Tabwera bro ." Fra anasiya zomwe amapanga ndikupita pomwe Luca's anakhala.
"Adha zabho , ndimafuna ndikupepese zomwe zinachitika ndipo Favour anandilankhula , ndiye ndaona Kuti Chikondi sakakamiza nkazi uja tengani ndipo tizikhala Ngati kale."
"Zikomo kwambiri ndakunyafika aseh ndiwedi b
Nchimwene wanga weni weni mulungu akudalitse."
"Osadandaura ndipo Favour ndimuuzaso."
"Zikomo kwambiri." Anagwirana dzanja.
Nthawi yomwe Lucas anamuimbilaso Favour ndimumupepetsa Fra Ali pomwepo ndipo ananvana .
Kenako Francisco anapita kukapitiliza zomwe amapanga.
Matsiku anayamba kuthela kuchitseko ndipo chikondi cha Favour ndi Francisco chinali chosangalasa Ngati love yamu film Koma ena samawaonela kukondwa.
Tsiku Lina Lucas anabwereka phone ya Francisco ananena Kuti akufuna atumize nyimbo.
Fra sanavute kupeleka poti amqmulemeleza kwambiri Luc's.
Luc's atatenga phone anapanga sikani WhatsApp ya Francisco ndipo inakhalaso mu phone mwake.
Zitatheka anakamubwezera mwini wake phone.
"Zatheka ?"
"Eya zinali za fast ."
"Oky chabwino." Nkhondo ndi anasi.
Lucas maso anali Kwa Fransisco, ataona Kuti phone sakuigwilitsa ntchito Lucas anamukhula Favour pa phone yake koma WhatsApp wa Fran
"Hey babe." Favour sanachedwe kupanda reply.
"Yes Hunny."
"Ndakusowa mami ndikufuna tikumane ."
"Mesa ndinakuuza Kuti ndili ndi ma assignment ambiri Fra iwe."
"Sukachedwa l promise."
"Ndasowa katundu wako."
"Ukulankhula zopusa waledzela katundu wake uti ?"
"I mean ndakusowa Koma Favour please."
Kenako FRA anatenga phone yake ndipo Luca anafufuta zinthu zina mu phone mwake.
"Oky ."
Message fra anaiona.
"Yes l'm oky." Francis anayankha akuseka amaonangati Favour walakwisa message.
"Oky tilankhulana ndimalize zomwe ndikupanga."
"Oky ."
Poti Francisco samafuna kumupatsa busy favour Za sukulu sanalankhulaneso mpakana madzuro anakwana.
Nthawi Ina itakwana Favour sanaimbe phone ananyamuka kupita komwe anauzidwa Kuti akumane ndi Francisco kuja.
"Ndafika?" Favour analemba message Koma tsiku limene Francisco samakhala busy ndi phone paja ukalodzedwa sununkha.
"Lowa mgalimoto ya blank babe." Munthu anayankha ndipo Favour analowa.
Atangolowa anadabwa zakuti FRA mulibe ndipo anamuika nsali kukamwa pomwe panali mankhwala ndipo Favour anakomoka.
______________
"Ndikufuna tipite kwasing'anga tikaone vuto ndi chani Za mimba Hope. , ndili ndi maganizo Za nkhani ya Favour pano mwezi wathaso Koma olo mimba."Nelson analankhura kuuza nkazi wake.
"Inetu zamakhwala ayi kwathu ndiopemphela."
"Ndikufuna mwana."
"Nelson zikuoneka Kuti ndili ndi mimbaso Ina mwezi Uno."
"Favour serious?"
Ikupitilira...
Share Nd comments
*Pangani search komaso like page ya N.Lady super stores Kuti musasemphane ndi nkhani zabwino komaso zosangalasa kuphunzitsa ndikulangiza*