19/06/2026
Good morning, lero pa 19 jun 2026 kugona kukuvuta ukaganiza MA BUS 55 +10 A BUSHIRI 65.
Amalawi kumayamikila ma Bus 55 is too much atithandiza ndipo atiganizila tosefe tipita basi kozekani .
Zikomo a APM komaso zikomo a Prophet Bushili ambuye azikudalisani APM ndi wamzelu kwambili ndani amayembekezela izi ?
Ine Okoma atani ndikuti zikomo nditha kugwada kuthokoza mwava kulila kwanthu.
Mundinkhululukile chifukwa ndimakuvutisani daily ndinali ndi chisoni kwambili potengela kuti naneso ndili south africa kokuno ndikuziwona ndimaso ndiye mutu sukugwila ndikhululukileni koma tathokoza.
SOPANO TIGAWE MA BUS:
Ma Bus 10 apite Pretoria osaiwala ku thembisa kumeneko kovuta ngati ku Durban.
Ma Bus 30 apite ku Durban kumeneko kuli anthu ochuluka omwe avutika kwambili kuposa kulikose.
Ma Bus 10 apite ku Johannesburg kumeneko mavuto sakuveka kwambili osaiwala ku Alexander.
Ma Bus 3 apite ku Pumalanga kumeneko kwavuta kwambili.
Ma Bus 2 apite ku PeterMaritzbug kumeneko sikukuveka zovuta kwambili.
Ma 2 apite ku westencape.
Ma Bus 1 ipite ku Eastern Cape
Ma Bus 2 apite ku tree state.
Bus 1 Limpopo.
Ma Bus 3 apite ku Capetown.
Tasala ndi ma Bus 2 omwe tasowa kopita nawo mukuganiza kuti ndagawa bwino? kapena ndalakwisa ? awili osalawa apite kuti ? Ndachulusa kuti? nanga ndachepesa kuti ziwani kuti awa ndimaganizo anga osati aboma koma zomwe tingayankhe zithandizila Bomalo kukhala chiwelengelo chabwino paja ife ndiamene tolikuno .
Anthu okhala madela odzungulila tantchulamo azipita komwe ayandikana nako.zikomo.
Follow Moto Salumpha
Tisaiwale kuthokoza Bushili komaso atupele muluzi ndi ena ose omwe atengapo gawo ife tithokoza bwino tikabwela.
19/06/2026
19/06/2026
18/06/2026