28/10/2022
Ku dziko la Britain
Mzungu wina analowa mu restaurant. Atalowa, anaona munthu wakuda atakhala pa corner pa restaurant yo.👨🏾
Mzungu uja anamuitana opereka zakudya kenako anakuwa ak*tulutsa mpuk*tu wa ndalama zake amvekere..."Ndimugulira aliyense zakudya muno!! Kupatula munthu wakuda wakhala apoyo!"
Opereka zakudya uja anagawa zakudya kwa anthu onse mu restaurant muja kupatula munthu wakuda uja.👨🏾 Mmalo mokhumudwa, munthu wakuda uja anamuyang'ana mzungu uja kenako anayankhula k*ti.."zikomo".
Izi zinamukwiitsa mzungu uja ndipo anatulutsa mpuk*tu winanso wa ndalama nakuwanso k*ti..."Ndimugulira aliyense botolo la chakumwa chilichonse chomwe akufuna muno kupatula mkada wakhala apoyo"👨🏾
Opereka zakudya uja anagawa zokumwa restaurant yonse kupatula munthu wakuda uja👨🏾. Munthu wakuda sanadandaule kanthu koma anayankhula mawu ok*ti.."zikomo".
Izi zinakwiitsa kwambiri mzungu uja, ndipo pompo anamuitana opereka zakudya uja k*ti amufunse funso. Atafika opereka zakudya, mzungu uja anamufunsa k*ti..."Kodi munthu wakudayo vuto lake ndi chani? Ndagulira aliyense chakudya ndi zakumwa muno kupatula iyeyo, mmalo moti akhumudwe akungosekelera kenako nkunena k*ti zikomo. ndi wamisala kodi?"👨🏾
Opereka zakudya uja anayankha nanena k*ti..."Ayi siwamisala. Iyeyo ndi mwiniwake wa restaurant yi"
Phunziro: Adani anu azakugwilirani ntchito yokomera inu koma iwo asakudziwa k*ti ak*tero.😊