Lifuwu Rice Research Station

Lifuwu Rice Research Station Lifuwu Experiment Station conducts
research activities on rice breeding
and agronomy

Brief Specifications of the Machine:- Rows: 6-row planting system- Fuel Consumption: 3-4liters of petrol per acre- Plant...
31/07/2026

Brief Specifications of the Machine:
- Rows: 6-row planting system
- Fuel Consumption: 3-4liters of petrol per acre
- Planting Speed: 1 acre completed in 30 minutes
- Seedling Height: Optimal at 12โ€“15 cm
- Plant Spacing: Adjustable between 16 cm and 23 cm
- Customization: Number of seedlings per station is calibratable
- Tray Capacity: Each tray holds 200 grams of seed
- Seed Requirement: 1 acre requires 60-80 trays

Tiyambepo transplanting fadah ๐Ÿ˜Š
31/07/2026

Tiyambepo transplanting fadah ๐Ÿ˜Š

17/07/2026

CHDZIWITSO
Moni alimi a mbewu ya mpunga uko konse komwe mulili.
Tafuna kukudziwitsani kuti pamene nyengo ya mvula yayamba kubwera kawandikira wandikira, pali atambwali ena amene akumagulitsa mbewu ya mpunga posintha maina a mbewu mozimbayitsa ndi kumanamanso za mmene mbewuyo imaberekera ndi mmene imachera .

Lifuwu Research ndi office yomwe imathandizidwa ndi boma pansi pa nthambi ya za kafukufuku wa mbewu ( Department of Agricultural Research -DARS).mu unduna wa zamalimidwe.

Ofesi yathu imagwira ntchito molumikizana ndi mabungwe komanso ma kampani a za mbewu ena monga kampani ya:
SEEDCO,CISP,AICC , ICRISAT kungotchulapo ena mwa Iwo. Ofesiyi imagwiranso ntchito ndi ma bungwe opanga bizinezi monga ma koparetivi, ma bungwe oyendetsa madzi mma sikimu ( Water Users Association) ,ma bungwe ovomelezeka ogula mbewu ndikumagulitsa mbewu kwa alimi anzawo( Seed growers Association), komanso bungwe la alimi loyima lomwe si la boma la NASFAM .

Mabungwe akunja omwe amatithandizira ntchito komanso upangiri ndi monga bungwe la za kafukufuku wa mpunga pa dziko lonse( IRRI) bungwe la za mbewu ndi ulimi ku Korea( KAFACI) bungwe la za kafukufuku wa mbewu za mpunga ku zambwe kwa Africa,( Africa Rice) komanso bungwe la za mbewu ndi chitutuko Cha mmaiko okwera kumene la ku Italy ( CISP) komanso bungwe lowona. za ma ubale ndi chitutuko la ku Japan( JICA)

Alimi musapusitsidse ndi atambwali omwe akumalemba zabodza zokhudza mitundu ndi misika ya mbewu ya mpunga mmasamba a mchezo muberedwa ndalama pogula mbewu yosavomerezeka.

Alimi a mchigawo cha pakati ndi kumpoto musadere nkhawa ndi kulengeza koyamba kokhudza ng'anba yomwe azanyengo analosera pakuti ulosi wa chiwiri ukuonetsa kuti ng', ambayi sikhala ya ikulu mzigawo ziziwiri.

Yambani kukonzekera pokonza mminda mwanu kuti mudzathe kugwiritsa ntchito bwino magwedwe amvula mdera lanu potengera mwai mvula yoyamba komanso kusankha mbewu yogwirizana ndi madera anu molongana ndi mulingo wa mvula yomwe idzagwe mmadera osiyana siyana.

Mbewu zonse zomwe zimalimidwa modalira mvula zilipo ku ofesi pa mtengo wa K10, 000 pa kilogalamu Sankhani mbewu yabwino yomwe imachita bwino malinga ndi magwedwe a mvula kumadera anu osiyana siyana..

CHENJEZO

kugulitsa mbewu yomwe a ofesi ya za kafukufuku sanaiyese komanso sanaivomereze ndi mulandu malingana ndi malamulo a ku boma.

Zikomo.

17/07/2026

Greetings from Lifuwu Rice Research Station.

Our office would like to inform all rice farmers across the country that there are some unscrupulous rice seed traders selling products bearing names almost similar to our products. We would like to let farmers be on alert in case they see such products in question on different marketing platforms

Lifuwu Rice Research Station is a government funded institution in the Ministry of Agriculture and Security, Department of Agricultural Research Services -DARS. Our internal collaboration include SEEDCO , International Committee for the Development of Peoples (CISP), Rice Cooperatives . Water Users Associations,Registered Rice Seed Growers, African Institute for Cooperate Citizenship(AICC) and National Small Holder Farmers Association of Malawi ( NASFAM) International Crops Research Institute for Semi Arid Tropics ( ICRISAT) . International Collaboration includes The International Rice Research Institute (IRRI) Korea Africa Food and Agricultural Corporation Initiative ( KAFACI) , Africa Rice formerly West African Rice Development Association ( WARDA) , Commitato Internazionale Per lo Sviluppo Dei Popoli ( CISP) and Japanese International Corporation Agancy ( JICA).

There are three technical sections namely Rice Breeding ( Breeders) ,Rice Agronomy ( Agronomists) and Seed Services Unit, ( SSU), a seed testing and certification satellite for International Seed Testing Association ( ISTA) accredited laboratory at Chitedze Research Station.

We would also like to advise farmers especially in the central and Northern regions not to panic with the impending El nino occurrence as dry spells won't be severe as initially predicted. Prepare rice fields early so that you will make the best use of rains your respective areas will receive especially sowing ( direct seeding/dibbling immediately after the first rains.
Duping farmers through misinformation and disinformation on product performance, nomenclature and reserve engineering is against rules by Competition and Fair Trading Policy in Malawi.

Basic Seed for almost all released varieties is available at K10,000 per kg Chose the best suited varieties that respond positively to prevailing weather conditions in your respective areas.

Regards

Winter rice farming preparations.Inu mwagaula kale fada?Osafooka๐ŸŒพ๐ŸŒพ๐ŸŒพ
19/06/2026

Winter rice farming preparations.
Inu mwagaula kale fada?
Osafooka
๐ŸŒพ๐ŸŒพ๐ŸŒพ

Mwakoma Nonse, tikuthokozeni Chifukwa chotsatira mwachidwi ulangizi wa mbewu ya mpunga  kuchokera kuno ku Lifuwu Rice Re...
12/06/2026

Mwakoma Nonse, tikuthokozeni Chifukwa chotsatira mwachidwi ulangizi wa mbewu ya mpunga kuchokera kuno ku Lifuwu Rice Research Station. Tikukhulupilira ndithu kuti pang'ono panzake mukupindura . Tithokozenso chifukwa Cha mafunso anu omwe akupangitsa kuti nafe tiziyenda ndi nthawi komanso kuzamitsa kafufuku wathu.

lero tikambirana za mmene mungapangire ma nazare anu mwa ndondomeko ngati munsimu.

1. KUSANKHA MBEWU.

-sankhani mbewu yanu kuchokera ku matumba omwe munasunga ndipo munalemba dzina la mbewu
- onetsetsani kuti komwe mukukatenga mbewu matumba a mtundu Umodzi wa mbewu anali malo amodzi . Osatenga mbewu kumalo osungira mbewu komwe matumba a mitundu yambewu zosiyana siyana anaphatikizana kapena kuti anaikidwa mwa chinansanganya.Chotsani njere zonse zomwe zili mphwepwa ndi zosiyana mmaonedwe ndi njere zna za mtundu wa mbewu imodzi.
- Kumbukirani kuti mbewu yokwanira ma kilogiramu 40 imakwanira hectare imodzi pamene ma kilogiramu 16 imakwanira ekala imodzi.

MALO A NAZALE.

-Malo a nazale akhale a thya thya thya (flat) , osati pena kukwera pena kutsika . madzi amakhazikika ndi kulowa pansi mofanana pamalo otelewa.
-Malo a nazare akhale komwe ziweto sizimafika ngakhale usiku. Ngati muli ndi mantha kumbali ya ziweto , mangani mpanda kuzungulira malo a nazale
-Onetsetsani kuti Malo a nazale ndi ofikirika nthawi zonse komanso madzi amafika mosavuta kapena kuti kutenga madzi ndi pafupi.

KUKONZA NAZALE

-unjikani zinyalala pa malo anazale ndipo zikauma ziwotcheni . izi zimathandiza kuti njere za mbewu zomwe zikadali mu dothi zife . Udzu ndi mpunga ongomera okha umapsyeranso limodzi mukaotcha. Phulusa lomwe latsala mutaotcha zinyasi ndi manyowanso.

-musaiwale zida ngati khasu, chingwe/linya, tepi , ma peg zifunikira pa ntchitoyi

-Gaulani malo a nazale pafupifupi phanzi limodzi mozama kupita pansi.

-phwanyani mauma/ mabuma/ magulumwa onse kuti malo akhale ndi tizigulumwa ting'ono ting'ono tomwe sitingavute kusungunuka
-Lembani makulidwe wa bedi .
Bedi limodzi likhale ma mita khumi mu litali ndi mita imodzi mu lifupi.

-Mabedi pafupifupi makumi awiri( 20) ndi okwanira pa hekitala imodzi ndipo Mabedi pafupi fupi 8 ,(asanu ndi atatu ) ndi okwanira pa ekala imodzi.

kuchoka bed imodzi kufika bed lina zitalikirane pafupifupi phanzi limodzi( ma sentimita 30) pamene kukwera kwa bed limodzi kukhale theka la phanzi lanu ( ma sentimita 15).
-Ka njira komwe mwasiya pakati pa bedi ndi bedi kamathandizira poongolera madzi komanso kuyenda mosavuta mukamagwira ntchito ya pa nazale.

-Thirani madzi pa ma bedi any kuti pafewe koma ngati panali pofewa kale , chinyezi chinalipo ndikhale ndiye kuti madzi mudzathira mukaika mbewu.

KUIKA MBEWU PA NAZALE.

-Ikani mbewu mu ka bigili , mbale kapena saka ndikumwaza bwino bwino pa ma bedi anu. onetsetsani kuti mbewu siinathithikane malo amodzi pa bedi . pofuna kupewa kuthithikana kwa mbewu, mwazani ndi manja mbewu yokwanira ma kilogiramu awiri( 2 kgs) pa bed iliyonse.
-kwilirani mbewu ndi dothi lotsala popanga ma bedi , mbewu isamaonekere mukaikwilira koma ngati ikuonekera , phimbirani ma bed anu ndi udzu kuopetsa mbalame kuti zingatoretore.

-wazani madzi a mulingo wabwino mutakwilira mbewu yanu kapena mutaphimbira mbewu yanu

-osaiwala kumadzathilira pa nazale kuti chinyontho chisamasowe pa nazale mbewu imere ndi kutuluka bwino. Kuthilira madzi pa nazare kumathandizanso kusungunura michere ya mmanyowa ndi feteleza.

MBEWU YOKUNDIKA.

Ngati mukufuna mukufuna mukaike pa nazale mbewu ya chimera tsatirani izi.

-ikani mbewu yanu mu ndowa / magiri womwe muli madzi okwanira
mbewu mu ndowa/ bigiri ikhalemo ma ola 24(tsiku limodzi) ili mmadzi.
Chotsani mbewu yanu mu ndowa/ bigiri ndikuilowetsa mmasaka .
Tsekani kukamwa kwa masaka ndi chingwe/ linya.
-kumbani dzenje / mayenje akulu bwino malinga ndi muyeso wa mbewu yomwe mukufuna kukafesa.
ikani mbewu yomwe ili mu saka/ thumba ija mu dzenje munakumba lija ndikukwilira / kufotsera bwino bwino.
-pakatha masiku osachepera awiri( 48 hours) , kaichotseni mbewu pa dzenje mukapeza yaphulika phulika , yapanga chimera mizu

10/06/2026

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Patrick Steven, Jennipher Phirisagawa, Agie Mwase, Khefie Kwendakufa Banda, Chicco Nthali, Jimmy Chindindindi Luhanga, Dickson Chimwanga, Fabiano Blanzioh Josaya, Fredrick Bandawe, Fanuel Zigwa, Chisomo Mazengera, Pungulani Micheal James, Master Maliro, Ahmed Sudais James, Beatrice Mthunzi, Osward Gandigandi-phiri, Chikondi Samuel Kapito, Diana M. Chirwa, Alex Mpando, Tony Shaba, Richman Goliath, Mercy Danielz Bwanali, Chitsanzo Njombwa, Shadrec Chigwenembe, Chimwemwe Tebulo, Constance Musopole, Clement Malangwasila, Umar Maulidi, Ali Kumtenga, Chibongah Jnr, Archangel Munthali, Afinda Alfred Afinda, Harvey AliLeo Ndindi, Isaac Chirwa, Collings Batison, Prosper Idris Dada, Felix Chilomo, Spencer Matandala, Kenneth Chipeta, Phady Lozo, Chikondi Chanthunya, Rล“ Se

๐ŸŒพ๐ŸŒพ๐ŸŒพ๐ŸŒพ
06/06/2026

๐ŸŒพ๐ŸŒพ๐ŸŒพ๐ŸŒพ

Moni Moni alimi a mbewu ya mpunga uko konse komwe muli. Lero pa 5 mwezi wa June ife azilangizi anu a mbewu ya mpunga Kun...
05/06/2026

Moni Moni alimi a mbewu ya mpunga uko konse komwe muli.

Lero pa 5 mwezi wa June ife azilangizi anu a mbewu ya mpunga Kuno ku Lifuwu Research mogwirizana ndi nthambi yazakakufuku wa ulimi wosiyana siyana MMalawi muno( Department of Agricultural Research Services -DARS), tinali ndi chionetsero Cha mbewu ya mpunga. Chilinganizochi chinakonzedwa ndi thandizo la thambi yopititsa patsogolo mbewu zomwe zangotulutsidwa kumene kuti alimi apindule ( Agricultural Commercialization- AGCOM.

Chionetserochi chinabweretsa pamodzi alimi a mmasikimu ndi ma koparetivi monga Koperetivi ya Limphasa, koparetivi ya Lifuwu,koparetivi ya Mkondezi komanso bungwe la alimi loyendetsa madzi mu sikimu ya Lifuwu. Akulu akulu ena ku chionetserochi ndi monga adindo osiyanasiyana a ku unduna wa za ulimi ku likulu ku Lilongwe, adindo ku ofesi ya za ulimi ya Salima ( ADD ndi RDP), oyang'anira malo a za kafukufuku a Mkondezi, Lifuwu Baka ndi Kasinthula. Mulendo wathu wamkulu pa chionetserochi anali wamkulu wa nthambi ya zakafukufuku muno MMalawi Dr Grace Kaudzu.

Alimi anatenga magawo angapo kuphatikiza kulongosola mmene akupindulira ndi ndondomeko yolandira mbewu ku ofesi ya za kafukufuku komanso kuthandizira potulutsa mbewu yomwe alimi eni ake ayikonda

Akulu akulu pa kafukufuku wa mbewu ya mpunga analongosola ndi kuyankha mafunso a mmene mbewu za nyuwani zikuchitira mminda mwa alimi maka pa zokolora ndi masiku omwe mbewu zosiyana siyana zimatenga kuti ziche.

Alimi adzionera okha mbewu monga Nunkile, Wachangu, Mtupatupa, kudya, Makafaci , Linga, Mthetsanjala, Nazolo, Uwemi, Kilombero ndi Zina zambiri zomwe mungalime kuwiri pa chaka kupatula Kilombero ndi Faya

Zikomo

Greetings from Lifuwu Rice Research. Today , 5th June 2026,Lifuwu Rice Research in conjunction with the Department of Ag...
05/06/2026

Greetings from Lifuwu Rice Research.

Today , 5th June 2026,Lifuwu Rice Research in conjunction with the Department of Agricultural Research Services (DARS) organized a field day under Agricultural Commercialization program (AGCOM). The field day drew participants from Limphasa Rice Cooperative, Lifuwu Rice Cooperative, Lifuwu Water Users Association, Lifuwu Seed Growers Association, Officials from Salima Agricultural Development Program, Salima Rural Development Program, Baka , Mkondezi, and Kasinthula Research Station and Director of Agricultural Research Services Dr. Grace Kaudzu.

Farmers took turns explaining how they are benefiting from Research to Farmer Seed. diffusion programs and being part and parcel in Participatory Varietal Selection whilest appreciating variety crop stand

Scientists and technicians also answered questions from farmers and other officials on performance( yield and maturity period).

Amongst the varieties showcased include ,Nunkile ,Mpheta,Nanzolo, Kilombero,Faya 14 M69 Katete, Kayanjamalo,Wachangu Makafaci,Kudya,Linga,Mthetsanjala and Mtutapa. All of them except Kilombero and Faya 14 M69 can be grown both in Winter and Summer.

Regards.

Address

Lifuwu Research Station , P. O. Box 102
Salima

Opening Hours

Monday 07:30 - 17:00
Tuesday 07:30 - 17:00
Wednesday 07:30 - 17:00
Thursday 07:30 - 17:00
Friday 07:30 - 17:00

Telephone

+265999362461

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Lifuwu Rice Research Station posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share