18/11/2025
Mr. Phiri: Achisaleπ£οΈπ£οΈπ£οΈπ£οΈ
Mr. Chisale : ine a Phiri mwaswera bwanji.
Mr. Phiri : Ndaswera bwino aise kaya kabaza akutheka ndi mvula yayambayi tisake ya feteleza komaso kusakiratu ka school fees kamwana.
Mr. Chisale : Mwayiwe bola ndikupeza yandiwo komaso ufa ndisaname Kaya Chaka Chino zitithera bwanji sindikudziwa .
Mr. Phiri: M'awa ija unayambitsa nkhani Kodi umati chani chifukwatu iwe sindikuona bwino ukatero wapeza mkazi wina paja akabaza amusalima kukonda akazi.
Mr. Chisale:ππππππππππ koma Phiri usandiseketse paja nkhani zanga zimakhala zoduka mitu nthawi zonse.
Mr. Phiri : ππππ nanga unandiuzapo nkhani yaphindu kupatula kundiuza za mkazi wa kwa mfuti uja komaso hule lako laku msangu lija .
Mr. Chisale : Aaaa koma Phiri wandionjeza aise wayiwala iwe wako waku mtukula mwendo komaso uja wa patakumana uja.
Mr. Phiri: Eya wandikumbutsa ndamva kuti pa Takumana pa Nazerene Church Pali Private Secondary Yatsopano akumaitcha Armor of God Private Secondary School anthu akuti kumeneku kokha maphunziro ake ndi abwino kwambiri osati ma private angoti mbwee ntauni muno.
Mr.Chisale : Aaa a Phiri Inetu mwana wanga Ali kale komko koma simomwe akukhonzeramo , ukumbukira ali form one amangolakwa ali secondary school ijayi koma anangoti wapita ku Armor of God Private Secondary School mwana wanga pano ndi mtondo ndipo sindikukayika mayeso a form 2 akhoza bwino kwabasi.
Mr.Phiri : Aaaa iwe ndiye bwanji nthawi yonseyi umabisa, osandiuza kuti nane akayambe komko chifukwa ndamva kuti fees yake ndiotchipa kupelekaso kawiri oti Ife akabaza sizingativute.
Mr.Chisale : Paja m'mawa uja umati ndimakuuza zoduka mitu koma ndimafuna ndikudziwitse za Armor of God Private Secondary School .
Mr.Phiri : πππ iwedi ndioduka mutu aise basi customer uyo amwene mwina tipeze ya fees.
Note: Places are available for January intake in all forms.
Contact us on 0996142447 for more information.