30/10/2025
MADEMO OOPSA ABVUTA KU TANZANIA
Okupasilani ine mlakatuli mwinimbumba Dicksan kasongo
Dziko la Tanzania lero kuli utsi wa teargas okhaokha mbali zonsezonse pamene achinyamata ambiri alowa mumseu kusokoneza chisankho chomwe msogoleri wa dzikolo mai Samia Suluhu Hassan akupikisana okha pa ballot. Achinyamata wa abudula ndi kuwononga ma ballot box komanso ma ballot papers ochuluka potsutsana ndi chisankhochi chomwe mai Samia Suluhu Hassan apezekapo pa ballot okhaokha boma litamanga otsutsa ambiri ndi kuwaletsa kuti asayimile nawo pachisankhochi. Otsutsa ena anaphedwa pamene ena anasowa tsiku la chisankho lisanafike nkomwe. Chadabwitsa kwambiri ndi chakuti boma la Tanzania lagwetsa internet komanso kuletsa atolankhani akunja kulemba nkhani zokhudza chilichonse chikuchitika mdzikomo.
A Samia Suluhu Hassan adali wachiwiri kwa msogoleri
John Magufuli yemwe adamwalira mchaka cha 2021 atangopambana chisankho cha 2020. Ngati wachiwiri kwa msogoleri wa dziko la Tanzania a Samia Suluhu Hassan adatenga mpando wa utsogoleri wa dzikolo monga mwa malamuro ndipo akhala akumalizitsa term yachiwiri ya a Magufuli. Chisankho cha 2025 chikupeleka mwayi kwa a Samia Suluhu Hassan kuti ayambepo kulamulira term yawo yoyamba monga mwa malamuro a dzikolo ngati angapambane pa chisankho chomwe akupikisana okhachiπ. Iwo akuyimila chipani cha CHAMA CHAMAPINDUZA chomwe msogoleri wake oyamba ndi Mwarimu Julius Kambarage Nyerere yemwenso ndi msogoleri oyamba wakuda wa dzikolo, ndipo sichinagwepo pa masankho mu mbiri ya dziko la Tanzania.
Uyuyu ndende ndichakwela analowa m'boma chifukwa cha mademo Koma Iwo analesa mademo anapha saulosi chilima kuteteza mpando wa u president
Anaseka ma account onse Peter muthalika Kuti alephele kupanga kampeni anamanga onse osusa Kuti aziopa
Amamanga olo anthutu osauka anapeleka maganizo awo powadzuzula
Democracy inatha zamphavu zinali zikwanje apolice ndiassilikali amaopa zifwamba zazikwanje Za Richard chimwendo banda
MCP sichipani Koma kagulu kauchifwamb