Happy new month, mwezi wakatemela wa HIV uwu tudziwa simungaphethile😂
SK. Health & Medics
Quality Healthcare for Every Life
28/06/2026
ZIKANG'A (HEEL FISSURE)
Kodi zikang'a ndi chiyani?
Zikang'a ndi ming'alu yomwe imachitika pakhungu lolimba la chidendene. Nthawi zina zimapweteka ndipo zimatha kutuluka magazi.
Zimene zimayambitsa:
• Khungu louma kwambiri.
• Kuyenda opanda nsapato.
• Kuyimirira kwa nthawi yaitali.
• Kunenepa kwambiri.
• Kusasamalira mapazi bwino.
• Matenda a bowa (fungal infection).
• Matenda a shuga kapena psoriasis.
Momwe mungadzisamalire kunyumba:
✅ Sambani mapazi m'madzi ofunda kwa mphindi 10–15.
✅ Pakani kirimu kapena Vaseline tsiku lililonse, makamaka usiku
✅ Valani masokosi oyera mukamaliza kupaka Vaseline ndipo chitani izi tsiku ndi tsiku kwamasiku osachepela atatu.
✅ Pewani kuyenda opanda nsapato.
✅ Pitani kuchipatala ngati ming'aluyo ikutuluka magazi, ikutupa, ikutulutsa mafinya kapena sikuchira.
SK. Health & Medics
Quality Healthcare for Every Life.
27/06/2026
ACNE VULGARIS (Ziphuphu)
Kodi ziphuphu ndi chiyani?
Ziphuphu ndi matenda a khungu omwe amachitika pamene mabowo a khungu amatsekeka ndi mafuta, dothi komanso mabakiteriya. Nthawi zambiri zimatuluka pankhope, pachifuwa, kumbuyo ndi m'mapewa.
N'chifukwa chiyani ziphuphu zimatuluka?
Ziphuphu zimatha chifukwa cha kusintha kwa mahomoni, mafuta ochuluka a m'khungu, mabakiteriya, komanso kutsekeka kwa mabowo a khungu.
Kodi mungasamalire bwanji khungu?
Sambani nkhope yanu kawiri patsiku ndi sopo wofatsa. Pewani kukanda kapena kufinya ziphuphu. Gwiritsani ntchito mafuta oyenera pakhungu ndipo muzimwa madzi ambiri. Muzidya zakudya zopatsa thanzi.
Kodi muyenera kuchita chiyani?
Ziphuphu ndi matenda ochiritsika. Ngati ziphuphu zikukulirakulira, zikupweteka kapena sizikuchira, pitani ku chipatala chapafupi kuti mukalandire chithandizo.
SK. Health & Medics
After HIV vaccine, fear Gonorrhea and other STIs
26/06/2026
In case you missed it, Katemela woteteza ku kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a AIDS ayamba kupelekedwa kuyambira pa 1 mwezi ukubwelawu malinganga ndi zomwe ministry of health yalengeza.
Mwina mukufuna akhale door by door? maganizo anu ndiotani😄
&Medics
28/11/2025
Malawi is expected to receive its first shipment of lenacapavir — a twice-a-year injectable HIV prevention drug — by the end of February 2026, offering a new addition to the country’s HIV prevention options.
National AIDS Commission (NAC) Chief Executive Officer Dr. Beatrice Matanje told MBCDigital that although Malawi was not included in the initial rollout, it has been assured a place in the second cohort under the PEPFAR programme.
She noted that the timeline will also depend on approval from the Pharmacy and Medicines Regulatory Authority (PMRA), despite the drug already receiving international clearance from the US Food and Drug Administration (FDA) and World Health Organisation (WHO) earlier this year.
So far, only Zambia and Eswatini have received shipments, each securing 1,000 doses from the US government.
Lenacapavir, administered twice a year, protects users by blocking HIV from entering healthy cells and offers long-lasting prevention without the need for daily ARV pills.
By Alufisha Fischer
18/11/2025
ANTHU ATATU AMWALIRA NDI NTHENDA YA MURBURG VIRUS KU ETHIOPIA.
Nduna yowona za umoyo m'dziko la Ethiopia a Mekedes Daba atsimikiza za imfa ya anthu atatu omwe amwalira kamba ka nthenda ya Murburg virus, kuchigawo chakum'mwera kwa dzikolo kufupi ndi chipata cholowera kum'mwera kwa dziko la South Sudan.
Malingana ndi zomwe yalemba Aljeezera News, pafufupi anthu 100 akusungidwa ku m'bindikiro (Quarantine) kamba koti akuganiziridwa kuti anakhuzana ndi anthu amene anamwalirawa.
Izi ziri chomwechi malingana ndi zotsatira zotsimikizika zakuchipatala cha m'dzikolo chatulutsa.
Ngakhale izi ziri chomwechi palinso chiwopsezo cha kufala kwa nthenda ya Ebola pamene anthu atatu amwalira ndi nthendayi ndipo enaso atatu akuonetsa zindikiro za kachirombo ka Ebola, pamene anthu 129 omwe ankhuzana ndi athuwa awayikidwa mu m'bindikiro.
Pakadali pano mayiko a Ethiopia ndi South Sudan ali pakalikiliki kulimbana ndi nthendayi ndicholinga choti isafalikire m'madera ena.
Wolemba: David Somba -Mzuzu
Source: Aljeezera News English.
Click here to claim your Sponsored Listing.
Location
Telephone
Website
Address
Mzuzu