05/10/2024
Mu Hadith ya Abu Huraira Rawah Imam Ahmad komanso Ibn Hibban yomwe Shaikh Alban ataifufuza adati ndiyaswahih, Anthu ena adati kwa Mtumiki 'Oh Inu Mtumiki, mzimai wina amaswali usiku onse swala zausiku ndipo masana amakhalira Kusala kudya, koma lirime lake limakhalira kunena zoipa za aneba ake.' Mtumiki adati IYEYO NDIWAKUMOTO. Ndipo anthuwo adati 'Ndiye Pali mkazi wina, amangoswali swala zokakamiza zija basi ndipo masana samasala kudya, koma lirime lake samakamba zoipa zaneba wake' Mtumiki adati IYEYO AKALOWA KUJANNAH.
Nkhani iyi ndiyoopsa kwambiri, tichenjere!! Kukhalira kukamba zobisika zaena, kufooka kwaena, kukhalira kukamba za anthu ena ndichinthu choletsedwa ndipo ndichinthu chomwe chikalowetse anthu ambiri kumoto. Mukukamba kwa Mtumiki madalitso ndi Mtendere zipite kwaiye adati ambiri akalowetsedwa kumoto chifukwa chalirime ndi maliseche awo.
Tsiku Lina Mtumiki adamuuza Muadh kuti SAMALA NDI LIRIME LAKO. Muadh adati 'Kodi tikafunsidwa pazomwe lirime limakamba Inu Mtumiki?' Mtumiki adati NDICHANI CHOMWE AMBIRI AKALOWERE KUMOTO AKUKHWEKHWEREZEDWA NKHOPE KAPENA MPHUNO ZAWO PANSI KUPOSA ZOKOLORA ZAMA LIRIME AWO?? A serious matter wallah! Intabih!!
Muhadith imene tsinde lake ndi Imam Bukhar komanso Muslim yomwe adaitulutsa Imam Tirmidh, Ahmad komanso Ibn Majah kuchokera kwa Abu Huraira ndipo Shaikh Alban adati ndi Hadith yoonadi, Mtumiki adati MUNTHU AKHONZA KUYANKHULA MAU, MAUWO NDIKUMUKWIITSA ALLAH NDIPO AKAMULOWETSA KUMOTO. ZIKATENGA ZAKA 70 ASADAFIKE PANSI PAMOTO. Pankhani zanzanu, samalani. Pankhani zaneba wanu, samalani. Mind your own business as much as you can, zimenezo ndizabwino kwainu kuposa kukometsa macheza pankhani zawina
Allah azititalikitsa kumchitidwe okamba zaena nthawi zonse!!