𝑨𝑹𝑨𝑴 𝑰𝑺𝑳𝑨𝑴𝑰π‘ͺ 𝑨π‘ͺ𝑨𝑫𝑬𝑴𝒀

𝑨𝑹𝑨𝑴 𝑰𝑺𝑳𝑨𝑴𝑰π‘ͺ 𝑨π‘ͺ𝑨𝑫𝑬𝑴𝒀

Share

QUR'AN Γ‘ SUNNAH

KUKUZA CHIKHULUPILIRO KOMANSO MOYO WABWINO
KWA
ACHINYAMATA A CHISILAMU

22/08/2025

Zinthu Zomwe Anthu Amakhumbakhumba Kuti adakazidziwa Ali ndi Zaka 20

1. Nthawi Ndi Chuma Chanu Chachikulu Kwambiri

Amapanga regret chifukwa cha kuwononga zaka zambiri pa zosokoneza, kusachita kanthu, ndi kuchedwetsa zinthu.
Phunziro:Yambani msanga; gwiritsani ntchito zaka zanu za m’ma 20 kumanga luso, kuphunzira, ndikusaka njira zopezera ndalama.

2. Umoyo Sungagulidwe Kachiwiri

Ambiri ananyalanyaza masewera olimbitsa thupi, kugona bwino, ndi kudya moyenera.
Phunziro:Samalirani thupi lanu tsopano; zizolowezi zomwe mumapanga lero zidzakhudza moyo wanu wonse.

3. Zizolowezi Za Ndalama Zimakhudza Tsogolo Lanu

Anagwiritsa ntchito mopitirira muyeso ali achinyamata ndipo anakumana ndi mavuto azachuma mtsogolo.
Phunziro: phunzirani za kasamalidwe ka ndalama msanga.

4. Maphunziro ndi Luso Zimatsegula Mipata

Ena sanatenge maphunziro mofatsa ndipo akupanga regret ndi mwayi womwe akuutaya.
Phunziro: Phunzirani mwakhama, pitirizani kuphunzira, ndipo mukhale ndi luso limene lingakupangitseni kukhala wofunika.

5. Kusankha Anzanu Olakwika

Anthu oyipa anawapangitsa kuwononga nthawi, kuchita zisankho zolakwika, kapena kuwafooketsa kuchita bwino.
Phunziro: Khalani ndi anthu abwino, olimbikira, omwe amakulimbikitsani.

6. Kusaphunzira kuchokera ku kulakwitsa

Ananyalanyaza kuphunzira kuchokera muzolakwitsa zawo.
Phunziro: Yesani zinthu zatsopano, zolakwika ndizabwino ngati mukuphunzira.

7. Kunyalanyaza Kukula kwa Maganizo ndi Malingaliro

Amazitenga olephera pa chilichonse ndipo sanali olimba mtima komanso sanali odzidalira.
Phunziro: phunzirani kukhala odzidalira.

8. Kusamanga Maubale abwino ndi Anthu

Anazindikira mochedwa kuti kupambana nthawi zambiri kumadalira amene mumawadziwa.
Phunziro:Pangani maubwenzi ndi aphunzitsi, akatswiri, ndi anzanu omwe ali ndi malingaliro abwino.

9. Kuwononga Nthawi pa Maubwenzi Opanda Tanthauzo

Ambiri anawononga mphamvu zawo pa maubwenzi oopsa kapena osapindulitsa.
Phunziro: yambani kudzikonza kaye; sankhani maubwenzi mwanzeru.

10. Kunyalanyaza Chikhulupiriro ndi Makhalidwe Abwino

Anapereka ulemu ndi makhalidwe awo chifukwa cha phindu lachidule ndipo anakhumudwa mtsogolo.
Phunziro: Khalani okhulupirika ku chikhulupiriro chanu, makhalidwe anu, zimabweretsa mtendere ndi ulemu wamoyo wonse.

11. Kusapanga Mapulani a Tsogolo

Anali ndi moyo tsiku ndi tsiku popanda zolinga ndipo anadziponya m’chipwirikiti mtsogolo.
Phunziro:Khalani ndi zolinga zomveka bwino ndiponso chitani pang’onopang’ono tsiku ndi tsiku kuti muzikwaniritse.

-TEAM

18/08/2024

AQEEDAH

Ndicho chiyambi chakuti munthu akhale pa njira yachisilamu yolondola

AQEEDAH

Ikangoti yaonongeka ndekutinso Chisilamu chamunthu chimakhalanso pa chiopsyezo

ANTHU AMBIRI

Akukangana Mmizikitimu kamba ka kusephana ma AQEEDAH

AQEEDAH

Ndi udindo Wa Msilamu aliyese kuyiphunzira

Na ngati amafuna atakhala Msilamu Wa bwino

18/08/2024

CHIYAMBI

Ndichimene chimafunikira kuti zithu ziyende bwino

CHIYAMBI

Chikakhala chabwino zinthuso zimayenda bwino

CHIYAMBI

Ukangoti wachiphonya ndekutiso ulendo wake umakhala Wa penapenda

22/07/2024

ASSALAAM ALYKUM WARAHMATULLAH WABARAKATUH

Ma LESSONS
Anayamba kuponyedwa

Join us today
0880658768

WHAT'S APPπŸ“žπŸ“ž

27/06/2024

TAJWEED FOR BEGINNERS

OPENING DATE:20th July 2024

OFFER'S
βœ“QAIDAH
βœ“AL-JAZAR
βœ“TAS-HEEL

AND MANY MORE!!!

COMPLETELY FREE πŸ†“ OF CHARGE

πŸ€

0880658768

07/06/2024

Ψ§Ω„Ψ³Ω„Ψ§Ω… ΨΉΩ„ΩŠΩƒΩ… ΩˆΨ±Ψ­Ω…Ψ© Ψ§Ω„Ω„Ω‡ ΩˆΨ¨Ψ±ΩƒΨ§ΨͺΩ‡
Assalaam alykum warahmatullah wabarakatuh

SECOND SEASON
Ma lessons athu anayamba ndi
Makhaarij Al huruf
Kulumikiza zilembo
Ma vowels
Zitsanzo
Mayeso
Izi zinaponyedwa ku gulupu loyambilila

Pamene ku gulupu lachiwiri kunali
Lahn
Huruf Al isti'ilaai
Ahkaam Raa
Ahkaam Laam
Zilembo ΨΈ & ΨΆ
Noon sakina wantanween

Ma video available on YouTube channel

for beginners

03/05/2024
19/04/2024

LESSON UPLOADED

JOIN US

# 0880658768

19/04/2024

Kodi QUR'AN imakuvutani kuwerenga??

Kapena musowa munthu wapadera okuthandizirani inu kapena ana anu
Kuwerenga Qur'an???

Musachedwe tijoineni
#0880658768

Ndipo simuzakhumudwa πŸŽ“βœ…πŸ‡²πŸ‡Ό

Want your school to be the top-listed School/college in Lilongwe?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Location

Category

Telephone

Address


Kauma
Lilongwe