20/02/2024
MALANGIZO PA NDEU
(1.) Ngati magwa mwangozi pansi,miyendo musamwaze kuteloko n'kutsekula chitetezo.
(2.)Ngati ukuona kuti sutha kuyimaliza ndewuyo mwayi wofuula ulipo musafinyike ndithu.
(3.)Anthu owonelera ndeu musawa dalire sangakulanditseni ndi Atolankhani amakhala akujambula zokayika pa ma status
(4.)Ngati mwapeza mpata wothawa musaope kuti anamwali akusekani,masukani kutelo ndithu maka muzithawa mukuona kumbuyo kuopa mwala.
(5.)Ndeu yomenya ma style idatha kale kale, m***a kumaponya zibakhela zachikwapa,bola musamale nzanuyo akazinda m***a kudzigwera nokha nokha.
(6.)Musachedwe ndi kumenya Karate,Judo, Kung-fu, Taekwondo, Jujutsu, izi zikudyerani nthawi gwiritsani ntchito fundo number (5.)
(7.) Please pa ndeu osatsekula kukamwa kuopa mnzakoyo kum'patsa maganizo oti aku thidzimule kukamwa.
(8.)Onetsetsani musatuluke magazi maka kukamwa Kaya kutupa pa mlomo kuopa kumutchukhitsa poyera yera mnzakoyo iye n'kutenga 3 points yonse.
(9.)Nkhakhale kubvula Malaya pandewu kumathandizira kuti poponya zibakhera manja azimasuka,komabe utha kuyiwala pothawa malayawo maka zikafika potentha zibakhela.
(10.)Mutha kuma yankhula or kulilima pandeu mawu owopseza uku mukuponyabe zibakhera cholinga muzimu patsa nthumazi mzanuyo.
(11.)Ndewu siyimanga mudzi siyabwino, mphamvu zomwe mukutayazo zipititseni kumunda mudzakolola dzinthu
(12.)Omwe akuku chemelelaniwo pandewuwo,ndiwo amakugwira kuti musathawe mnzanu mukumenyana nayeyo atagwa n'kukuferani.