*KUSAMALA ANA AANG'ONO A BABY CLASS, NURSERY, RECEPTION NDI ENA ONSE*
Ndi udindo wa sukulu kukhala ndi aphunzitsi komanso osamala ana omwe ali ndi chidwi komanso odziwa ntchito yophunzitsa ndi kusamala bwino anawo.
*Pamayenera kukhala njira ndi machitidwe oteteza mwana ku ngozi komanso kudwala kuno kusukulu.*
Ife ngati sukulu timazindikira ntchito yathu ndipo timayesetsa kupewa ngozi ndi kudwala komwe kungachitike pamene tikulera anawa.
*Tsiku lina ngozi imachitika ndithu ngakhale timasamala ingakhale kunyumba kwanu Inu muli pompo chifukwa palibe amene angapewe tsoka.*
Nthawi Zina ana amatha kuvulala posewera kapena mwana wina kuvulaza mzake chifukwa Cha mphulupulu monga ana omwe sakudziwa chomwe akuchita.
*Aphunzitsi samaonerera makhalidwe a ana aang'ono omwe akuyika pa chiopsezo ana anzawo koma mwachangu timawadzudzula ndi kulankhula ndi Makolo kuti nawonso atengepo mbali khalidwe loyipalo lisanakule*
Nthawi yosewera , ( play time) ya ana a ku nursery, reception ndi baby class ingakhalenso akuluakulu aphunzitsi amawayang'ana anawa akumasuka kuseweretsa ma toy komanso kupanga masewera osiyanasiyana paokha. Ndi zosatheka kuti mphunzitsi angamakhale pambuyo pa mwana pamene akusewera ndi cholinga chomuteteza koma amakhala akuyang'ana momwe ana akuchitira masewera awo.
*Nthawi yosewera yomweyi zimatheka mwana wina kugwa yekha ndi kuvulala .Wina angathenso kutsina mzake kapena kumukala kumaso.Wina angathenso kumugwetsa mzake mwangozi.Wina angathenso kuzivulaza yekha chifukwa Cha kusamva zonena aphunzitsi.* ZONSEZI ZIMATHA KUCHITIKA NDIPO APHUNZITSI AMAYENERA KUDZUDZULA OCHITIRA MZAKE ZOIPA KOMANSO KUPHUNZITSA ONSE MAKHALIDWE ABWINO.
Nthawi Zina mwana amatha kuvulala posewera koma aphunzitsi osadziwa chifukwa mwina ndi Malo osaonekera komanso mwana kapena anzake sadanene za kuvulala kwake . Aphunzitsi akazindikira za kuvulala kwa mwana amayenera kudziwitsa Makolo mwachangu pa foni zawo koma ngati sadadziwe nthawi Zina timamva Inu mukudandaula pamene ife siti
Yankho Elementary School
Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Yankho Elementary School, Elementary School, Lilongwe.
*NDALAMA YOLEMBERA MAYESO A KUTHA KWA TEREMU NDI K3,000
*Aliyense adziyenera kupeleka ndalama imeneyi kuti apangilidwe mayeso pakutha pa teremu.*
Ndalamayi idzipelekedwa ndi aliyense kuphatikizapo omwe adapeleka fizi zotchipa za pa Chaka Kaya ma term awiri.
*Ngati ophunzira sadapeleke ndalama za mayeso ndiye kuti salemba mayeso. Ife tizidikira Inu mukamaliza kupeleka fizi , mudzitha kupeleka ndalama ya mayeso.*
*Aliyense adzakhale atapeleka ndalama ya mayeso pasanadutse pa 5 march*
```*Mu Nyengo ino pemene ndalama ya Kwacha yagwetsedwa mphamvu ndipo zinthu zonse zakwera mitengo, sukulu yanthu yaganizirabe Makolo ndi ophunzira anthu. Sitidakweze fizi ngakhale kwacha yagwa komanso kuthandiza anthu ndi mafizi otchipa kwambiri kwakhala kukupitilira ndipo tikhala tikuthandizabe polora ophunzira kumalipira fizi zotsika kwambiri zogwira ntchito Chaka chonse.*```*
25/01/2024
Click here to claim your Sponsored Listing.
Location
Category
Telephone
Website
Address
Lilongwe