19/07/2026
TIYENI TIONE ZA LEMBO LA 'L' KOMANSO 'R' M'CHICHEWA
Malembo awiri amenewa ndi ena mwa malembo omwe amalakwitsidwa kwambiri m'kalembedwe ka Chichewa.
Pali malamulo angapo omwe amatsatiridwa pa kalembedwe ka malembo awiriwa. Tiyeni tioneko limodzi mwa malamulowa.
Nthawi zambiri, 'l' amayenera alembedwe patsogolo pa 'a', 'o' kapena 'u'. Pamene 'r' amayenera kulembedwa patsogolo pa 'e' komanso 'i'.
Tikuyenera tidziwe kuti m'mawu ena, lamuloli silitsatiridwa.
Mchithuzichi, muli uthenga omwe alemba ndi Mikozi, titha kuona kuti 'l' sadagwiritsidwe ntchito moyenera. Mwachitsanzo, alemba kuti 'kuthandizila' m'malo molemba kuti 'kuthandizira'.
Ndi mawu ena ati omwe alembedwa mosatsatira lamulo taphunzirali? alembeni mu comment box tiwone ngati mwaphunziradi😃😃
Pangani follow tsamba lino kuti muphunzire zambiri