16/05/2020
Muli bwanji okondeka mkulandileni pa tsiku linanso labwino lomwe tikakhale tikugawana Mau Amulungu pa mutu oti,
Mzelu ya satana imabwela ngati yokoma,
Hallelujah , mzelu ya satana okondeka imabwela ngati ndi yokoma,
tamvela , tikamati ichichi chimakhala ngati chinja kumakhala kungofanizila sikuti chimakhala cha original ayi, chomcho mzelu ya satana imangokhala ngati yokoma koma siyokoma konse ayi,
Genesis 3 kuyambila ves yoyamba , bilble likufotokoza za kuchimwa koyamba kwa munthu,
Itafika njoka kumupeza mkazi akuthyola zipaso, njoka inafunsa kuti, kodi anati musadye zipaso za mundamu? Ndipo mkazi anati ayi mulingu anati tidye koma chipatso cha mtengo wapakatiwo tisadye chifukwa tizafa tikazadya, njoka ikuti ayi kufa simuzafa , Mulungu akuziwa kuti tsiku lomwe muzadyelo muzafana naye.
Hallelujah, mzanga anthu ambili angwa mmavuto mu njila yotele , achinyamata ena pano mitu yawo siigwila chifukwa anamizidwa kuti akasuta chamba azakhala amzelu,
Ena lelo lino , ali ku Ndende , atanamizidwa ndi amzawo kuti ngati akufuna kuti asamavutike ayabe katangale ,
Ndikuti ena lelo lino mabanja anatha, ananamizidwa ndi amzawo , kuti ngati akufuna ku njoya mmoyo apeze wina wa pambali, chowawa kwambilinso ka chibwenzikonso kanawathawa.
Nde Mulungu akuyendela mmunda akuitana Adam uli kuti , akuti ndili pano ndavala masamba ndili wamaliseche,
Wadya Adam chipaso nnati usadye? Adam akuti mkazi ndiye wandinyenga, naye mkadzi akuti njoka ndiyo,
Satana ndiye anandinyenga, mundikhululukile bambo, satanandiye anandinyenga mindikhululukile si mzabanso,
Hallelujah, ambili Timazindikila zithu ziyavuta kale chifukwa sitikhala mmawu a Mulungu, Tamvela , lelo lino ena ambili akulila , ku Ndende, akulila ku zipatala , anazindikila kuti nsi satana zithu zitavuta kale,
Mukakhala mmawu okondeka ngakhale atabwela ndi zokoma njelekeze inuyo muzamugonjesa, m'bale tatiye tingotenga aka tigulise tipeze ya mmemo mmawa, chifukwa muli mu mawu, muzamuyakha , Bible limati usabe,
Amayi ndikuti mukakhala mmawu amzanu aja muzawauza bible limati usachite chigololo.
Mutakwanisa kuwapewa mu njila yotele sazabwelanso kuzasokoneza.moyo wanu , munga Bible linenela pa bukhu la Yakobo 4 v7 potelo mvelani Mulubgu ndipo mkanizeni njelekezi ndipo iye azakuthawani,
Mzelu ya satani imabwela ngati ndi yokoma , koma kumapeto kwake kumakhala misonzi yochuluka , nkhalani osamala , ndi ochenjela pa kuyenda mmau a Mulungu nthawi zonse ndipo Muzapambana , Amen