27/06/2026
Umu ndi m'mene ulimi wa tomato, anyezi ndi mbatata uja wayendera pofika lero!
Kuyesera ulimi kwambiri pogwiritsa ntchito zipangizo zachilengedwe ndi zina za lokolo.
Cholinga changa ndi chofuna kudziwa ngati ndizotheka kupeza njira zomwe winaaliyense akhonza kupezera chakudya mosavuta ndi ndalama zochepa kwambiri.
💡
1. Fetereza wa masamba a futsa, ndowe, mikozo ndi makoko a nthochi (BIOFERT-T1 “Chiuta-TdMa”)
2. Mankhwala othanirana ndi tizilombo m'munda a masamba a futsa, adyo (garlic), ginger, tsabola ndi soda ophikira (NAT-PESTCIDE T1)
3. Fetereza wa masamba a futsa ndi ndowe ngati manyowa, kuthilira ndi madzi a makoko a nthochi kuphatikiza ndi mikozo (BIOFERT-T2 “Chiuta-TdMa”)
4. Mankhwala othanirana ndi tizilombo m'munda a masamba a futsa, masamba a mpoza, adyo (garlic), ginger ndi tsabola wamuwisi (NAT-PESTCIDE T2)
📃
Zikuwonetsa kuti ndizothekadi kulima mbewu zakudya ndi ndalama zochepa kwambiri pogwiritsa ntchito zipangizo zachilengedwe-zalokolo.
Zinawonetsa kuti masamba a futsa amathandiza ku mbali zonse; kukulitsa ndi kuteteza mbewu ku tizilombo.
Komabe pali zopinga zomwe anthu ena ambiri sangathe kukwaniritsa kuthana nazo koposa kugula ku msika;
1. Zotenga nthawi kusiyana ndi kugula ku msika
2. Zowoneka zosagwira
3. Zosasilirika
4. Zowoneka zawumve
5. Zowoneka zamisala
6. Mapezekedwe a zinthu zina akhonza kukhala ovuta m'madera ena
M'malingana ndikuti anthu ambiri zinthu , komanso zolandira, ndipovuta ambiri kugwiritsa ntchito zipangizo zachilengedwe-zalokolo.
M'mwezi wa March 2026, ndinapeza kuti zachilengedwe, zopezeka nkhalango ndi luso la zachikhalidwe zathu timaziwona zosathandiza ndi zobwerera m'mbuyo. Izi zimachitika chifukwa zachilengedwe zimatenga nthawi komanso kawiri kawiri sizipananganika chifukwa sizifanana kweni kweni.
Kumbali yanga, chopinga chachikulu chomwe ndachiwona ndi kupitilira kopezeka kwa tizilombo tina makamaka mu tomato. Zopinga zonsezi zandipatsa chilimbikitso chokhazikitsa “ ” komanso nyumba yosungira mbiri ya zochitika za tizilombo topezeka m'munda ( , largely a ).
3rdworld Xplorations
George Goliati
Ili ndi gawo limodzi la ulendo umenewu wa Xpeditions 2030, osunga mbiri poyera kudzera pa makina a Artificial Intelligence (AI), ya zochitika pa moyo wa tsiku-ndi-tsiku m'Malawi ndi kuyeselera njira zogwiritsa ntchito zipangizo zachilengedwe-zalokolo munjira zawukadawulo zosafuna ndalama zambiri.
Cholinga changa ndi chofuna kudziwa ngati ndizotheka kukhala moyo watanthawuzo, waumodzi ndi opanda nkhawa kugwiritsa ntchito zipangizo zachilengedwe zawukadawulo zopanga tokha kudzera pa makina a AI. "...kufuna kudziwa ngati aMalawi tili ndi mzeru kapena ngati tili zilengwa-lengwa chabe."
Pofuna kuyankha funso ili, ndikufuna kuyesera kukhazikitsa midzi yochitira malonda osintha zinthu ndi kuzunguliza phindu (the Circles) pogwiritsa ntchito njira yochitira malonda odalirana ndi oyeselera mowonetsera—yomwe winaaliyense akhonza kufufuzira, kudziwira kapena kupezera zinthu zofunikira mosavuta, yomwe ndikuyitcha “comp@ss”.
🧭 Discoveries & Insights
https://docs.google.com/document/d/1qk3wTcAIGhMYlwRbBhezuZAJXAKqU9J_kc2sxPNxeZQ/edit?usp=drivesdk