15/06/2026
Mtsogoleri wa chipembedzo cha makolo cha M'bona, mfumu yayikulu Ngabu, ya m'boma la Nsanje, wati M'bona ali ndi kuthekera koletsa kapena kuchepetsa mphamvu ya nyengo ya El Nino yomwe ikhoza kukhudza dziko lino ngati aMalawi angathire nsembe kwa iye ndi chikhulupiliro.
Mfumuyi yati; "anthu atagwirana manja kupita ku Khulubvi kukathira nsembe ngati chikhulupiliro tili nachodi, kupempha M'bona mwini wake amene amadziwa zonse kudzera kwa Mulungu, vuto la ng'amba likhoza osadzakhalapo kapena losapyola muyeso.
Iyo yauza Zodiak Online lero kuti; "tikaona kuti nyengo yafika povuta timagula kachaso wathu ndi zina ndi zina kupita ku Khulubvi kukagwadwa ndikupempha M'bona kuti atithandize ndipo amatithandizadi," yatero mfumu yayikulu Ngabu.
Mkulu wa nthambi yoona za nyengo, Dr. Lucy Mtilatila, anauza Zodiak Online posachedwapa kuti pali kuthekera kwakukulu kuti dziko lino likumana ndi nyengo ya El Nino mu nyengo ya dzinja ya chaka chino.
Uku ndi kutentha kwa madzi ku nyanja ya mchere ya Pacific komwe akuti kumadzetsa vuto la kuchepa kwa mvula maka m'madera a m'chigawo chakumwera.
15/06/2026
Amalawi okwana 645 anyamuka lero kuchokera ku South Africa pa ma bus 8 kubwera kuno kumudzi ndipo afika lachitatu.
M'neneri mu unduna woona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena a Charles Nkhalamba, wauza Zodiak Online lero kuti awa ndi aMalawi omwe akuthawa nkhanza zomwe nzika za dzikolo zikuchitira anthu obwera ndipo anali pa msasa ku Durban.
A Nkhalamba ati chiwerengero cha aMalawi omwe akufuna boma liwathandize chaposa 7,000 tsopano, ndipo boma lipitiriza kutumiza ma bus okatenga anthu ofuna kubwera kumudzi kuno.
13/06/2026
Manda a Chilima ku Msipe Ntcheu 🕊️
13/06/2026
Iyi ndi nyumba ya chiliza (mausoleum) imene yamangidwa pomwe anaikidwa Saulos Chilima ku Ntcheu ndipo mwambo otsegula chilizachi uli m'kati panopa.
Continue Resting in eternal peace 🕊️
12/06/2026
South Korea opened its 2026 FIFA World Cup campaign with a 2-1 comeback win over Czechia in a Group A match at Estadio Guadalajara in Mexico on Friday (Korean time).
After a scoreless first half, Czechia struck first through Ladislav Krejci in the 59th minute to take a 1-0 lead.
South Korea responded in the 67th minute when Hwang In-beom found the equalizer, before Oh Hyeon-gyu completed the turnaround with the winning goal in the 80th minute.
With the result, South Korea secured its first victory of the tournament and collected three points in Group A, while Czechia opened with a defeat.
The Taeguek Warriors will next face Mexico, one of the host countries, which ranks No. 15 on the FIFA rankings, again at Estadio Guadalajara on June 19.
12/06/2026
Mexico yayamba bwino mu 2026 FIFA World Cup pamene yasosola South Africa ndi zigoli ziwiri kwa duuu (2-0) pamasewero otsegulira mpikisanowu Lachinayi.
Julián Quiñones (9’) komanso Raul Jimenez (67’) ndi omwe achita chipongwe Bafana Bafana kuti iwone tsoka 2 kwa chilowere pa masewero ochititsa kaso.
Masewerowa kunali ma Red Card ochuluka kuposa zigoli, Sphephelo Sithole (49’) ndi Themba Zwane (79’) a South Africa kuyaka m’chigawo chachiwiri komanso César Montes wa Mexico kulandira yake red card (90+2) kupereka zokamba kwa ambiri za umo mpikisano wayambira.
11/06/2026
Ku South Africa kwavuta eish!
10/06/2026
Mwaswerako bwanj madzulo ano Mzika?