Hope Atekwene Duncan Kesiya

Hope Atekwene Duncan Kesiya Jesus Christ loves us all repent come to Him.

20/11/2024

Uthenga wathu Lero Habakuku 2:2-3 verse 2 Ndipo Yehova anandiyankha nati lembera masophenyawo, nuwacenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira. 3 Pakuti masophenyawo alindira nyengo yoikiridwatu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama akacedwa uwalindire popeza afika ndithu osazengereza. Amen Abwezi sachedwa safulumira tiyeni tizidalira Mulungu wathu osakhumba zomwe sanatipase munthawi yake amen.

19/11/2024

Uthenga wathu lero ukuchokera pa 2Mbiri 1:1-15 ndipo verse 10 Mundipatse tsono nzeru ndifuna cidziwitso, kuti ndituruke ndifuna kulowa pa maso pa anthu awa,pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri? Amen okondedwa mfumu Solomo inapempha nzeru osati chuma tichurukirenji abwezi opempha chuma kwa Mlengi malo mwa nzeru. Ambuye atithandize tifune ufumu wake tisanayambe kufuna zinazo amen.

18/11/2024

Uthenga wathu lero ukuchokera pa Miyambo 12:1-28 verse 4 Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake, Loma wocititsa manyazi akunga cobvunditsa mafupa a mwamunayo 14 Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace, zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa our. Amen ndikufunirani tsiku lopambana alongo ndi abale nonse.

16/11/2024

Ndiwerenga nanu lero You 13:1-28 ndipo 4 akuti Koma inu ndinu opanga zabodza, asing'anga opanda pace inu nonsense 13 Khalani cete ndilekeni kuti ndinene condifikira cifike. Haleluya tichulukirenji okhulupilira anthu abodza kuposa kukhulupira Mulungu yemwe amapereka moyo kwa abodzawo m'bale siya kukhulupira anthu abodza bwera kwa Yesu zonse zaulere angofuna mtima wako ubwere pa maso pake moyera mtima amen. Happy Sabbath brothers and sisters.

15/11/2024

Uthenga wathu mmawa uno ukuchokera PA Mlaliki 3:1-22 verse 1 Kanthu Kali konse Kali ndi nthawi yace ndi cofuna conse ca pansi pa thambo ciri ndi mphindi yace .malemba akutiuuza momveka bwino kuti chilichonse chili nthawi yake choncho okondedwa tisamadera nkhawa pomwe zina zikuoneka ngati sizikuyenda izitu zimatanthauza kuti nthawi yake sinafike choncho tiziyenda kulimbikabe mwa Yesu tsiku lina tidzakhala mboni amen.

14/11/2024

Uthenga wathu lero ukuchokera pa Miyambo 20:1-30 verse 1 Vinyo acita ciphwete cakumwa caukali cisokosa.Tichulukirenji wochita zoonanga thupi masiku ano mudzina loti tikujoya m'bale siya za dziko bwera kwa Yesu nthawi yatha amen.

13/11/2024

Uthenga wathu lero ukuchokera pa Ahebri 10:1-38 ndipo verse 25 akuti Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amacita ena, komatu tidandaulirane, ndikoposa monga momwe muona tsiku lirikuyandika. Okondedwa nthawi yatha ndipo tili munthawi yoonjezera tiyeni tilape machimo athu ndikuyendesa ndi Yesu khristu nthawi tasala nayoyi amen.

11/11/2024

Masalimo 94:17 Akadapanda khala thandizo langa Yehova,moyo wanga ukadakhala kuli chete. Tipemphere zikomo Mulungu wanga poti munandipasa extra time munthawi yomwe ndinakumana ndi ngozi yoopsya kwambiri komatu inuyo Mulungu chinakukomerani kundisiya ndi moyo kuti ndilape zonyasa zanga zikomo Mulungu pa ichi ndidzalemekeza dzina lanu nthawi yonse ndili moyo amen.

10/11/2024

Uthenga wathu lero ukuchokera pa Masalimo 91:1-16 verse Popeza udati, Inu Yehova ndinu pothawirapo pants! Udaika Wam'mwambamwamba cokhalamo cako. Tipemphere olemekezeka inu Mulungu wathu tikuti zikomo poti chakukomerani kuti kutidzusa ndi moyo mukalemekeze Atate wathu, tikupemphani chitetezero mutsiku ili mudzina la Yesu khristu amen.

09/11/2024

Uthenga wathu lero Habakuku 2:1-20 verse 15 Tsoka wakuninkha mnzace cakumwa, ndi kuonjezezako mankhwala ako ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi so!. Hallelujah happy Sabbath beloved ones.

Address

Thyolo District Hospital Box 21, Thyolo
Blantyre

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Hope Atekwene Duncan Kesiya posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share