05/05/2022
TIYENI TIMUFUNSE YESU MWINI ATIUZE ZOONA
Kwa nthawi yaitali takhala tikutsutsana pa nkhani ya Yesu.Ndipo tinaganiza kuti ndi bwino kuti timve zoona zenizeni kuchokera kwa Yesu mwini wake.Ndipo iye anapereka mayankho momveka bwino motere:
Ndaona Malemba: Kodi a Yesu ndinu ndani?
Yesu: Ndine munthu(Yohane 8:40)
Ndaona Malemba: Kodi m***a kuchita chilichonse?
Yesu: Ayi,sindingathe kuchita kalikonse mwa ine ndekha(yohane 5:30)
Ndaona Malemba: Kodi ndinu Mulungu?
Yesu: Mwatani kodi,ndakuuzani kuti ndine munthu(Yohane 8:40)ndiye ndikhalanso bwanji Mulungu? Ine ndi mneneri wa Mulungu(Mateyu 13:57)
Ndaona Malemba: Ayi,Yesu koma ambiri amati ndinu Mulungu.
Yesu: Ayi,ine ndine mneneri wa Mulungu(Luka 13:33)
Ndaona Malemba: Nanga iwo amene amati ndinu Mulungu amakunamizirani?
Yesu: Iwo amene amati ndine Mulungu amapembedza mwachabe,ndipo chiphunzitso chawo ndi chochokera kwa anthu osati kwa Mulungu(Mateyu 15:9)
Ndaona Malemba: Nanga bwanji anthu amati ophunzira anu monga Paulo munawauza kuti ndinu Mulungu?
Yesu: ine? komanso anakuuza kuti Paulo ndi ophunzira wanga ndani? Ngati mukufuna kudziwa choonadi funsani ophunzira anga monga Petulo ndi ena aja.
Ine chabwino ndikukafunsa kwa Petulo,sindikufunanso chilichonse kuchokera kwa Paulo.
Ndaona Malemba: Petulo,eti Yesu ndi ndani?
Petulo:Yesu ndi mneneri wa Mulungu,ndipo Mulungu anachita zambiri zamphamvu ndi zodabwitsa kuzera mwa iye(Machitidwe 2:22)
Ndaona Malemba: a Petulo ndili ndi zambiri zoti ndikufunseni.
Petulo:Bwanji tidzakumanenso tsiku lina,chifukwa ndikuthamangira kumtundaku mkulu winawake dzina lake Paulo akuuza anthu zomwe Yesu sanaphunzitse,iye akufuna kusocheretsa anthu(Agalatiya 2:11)