02/12/2024
PHUNZIRO LA TAUHEED/AQEEDAH
LESSON # 3
pambuyo potchula zamitundu ya tauheed tatiyeni tifotokoze mwachidule kwambiri za mtundu ulionse paokhapaokha koma tiyambe ndi tauheed al rubúbiyah
1.Tauheed al rububiyah
kumenekot ndi kuvomeleza zot Allah ndiwayekha, ndiolenga chilichose chaziko lapansi komanso uye ndioyendesa kalikose, opereka moyo ndi imfa, odyesa.
ndipo kuvomeleza mtundu umenewu ndikwachibadwi ndithu ndipo simuzapeza mibado yapitayo k*ti imakanira za ntundu umenewu ayi, ngat mene wayakhulira Allah mu Qur'an kt
ولئن سألتهم من خلق السموات والارض ليقولن خلقهن العزيز العليم
mutat mwafuse kt kod ndindani amene adakenga kumwambi ndi nthaka azayakula kt amene adalenga ndi wamphamvu oziwa (Allah).
ndipo ma ayah onga awa alipo ambir mu Qur'an, mupeza kt Allah ak*tchula zama mushrikeenah k*ti amavomeleza k*ti Allah ndimwini kulenga, kupereka moyo ndi imfa, kudyesa ndizina zambiri, ndipo palibe amene adakanira zamtundu umenewu kungopatula kagulu kochepa chabe kawathu koma pansi oamtima akuvomeleza, kukanira kwao kumakhala chifukwa chozikweza.
timagulu tina topotoka mudini timakanira zoti ma mushrikeenah sanali kuvomeleza tauheed al rububiyah ngakhale pangono ndipo amaperekera umboni mayah monga awa
أفلا ينظرون إلي الإبل كيف خلقت والي السماء كيف رفعت والي الارض كيف سطحت
surah al qhashiyah: Kodi inu simungaone ngamila mene idalengedwera?, komanso kumwamba menee kudanyamulidwira(kukwezedwa), komanso men nthaka inayalidwira?
قَالَ مَنْ يُحْيِي الْعِظَامَ وَهِيَ رَمِيمٌ
adat kodi ndindan amene angaukise(angapereke moyo) mafupa ali ofumbwa?
وَقَالُوا مَا هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا الدُّنْيَا نَمُوتُ وَنَحْيَا وَمَا يُهْلِكُنَا إِلَّا الدَّهْرُ ۚ
ndipo adat palibeso umoyo wina kungopatula umen ife tiliwu tizafa komanso kukhala moyo, palibe chimene chimationonga ife kungapotula nthawi basi
فَقَالَ أَنَا رَبُّكُمُ الْأَعْلَىٰ
ndipo(pharaoh) adati ine ndimbuye wanu wapamwamba
ndima ayah ena amene iwowo amaperekera umboni
Alhamdulillah maulama adayakha kale iz ndipo tatiyeni tiziyakhe mwachidule kwambir koma momveka.
ma ayah amenewa akukamba zokukanira kwawo pankhani yakuukisidwa manda ndik*tiso akalipidwa ku akhirah, komanso akukana zoti palibe umoyo wina pambuyo paumoyo umene tiliwu, osat akukana zoti Allah ndiolenga, odyesa komanso opereka imfa iyayi.
k*ti muone ma ayah amu surat ghashiyah wo muona zoti Allah akuwafotokozera k*t aione ngamila komanso ndizina zimene atchulazo kt Allah anazilenga bwanji? ngat anakwanisa kuklenga zimenezo akakanike kupereka moyo kachikena? ndipo Allah anarchula zangamila chifukwa ndichinyama chimene chinali chachikulu chimene ma quraish(aluyah) amaweta anali nacho pafupi.
ndipo ma ayah amene akufotokoza za pharaoh sik*t iyeyo amakana ndi mtima onse ayi koma kunali kuzikweza pambuyo pot mtima umavomeleza ndithu, umboni wake ndikuyakhula kwa Allah koti
وَجَحَدُوا بِهَا وَاسْتَيْقَنَتْهَا أَنْفُسُهُمْ ظُلْمًا وَعُلُوًّا ۚ
ndipo adakana koma mitima yawo ili ndichisimikizo (ikuvomelez) ndithu, mopondereza komanso kuzikweza.
ndipo mukamvesesa zimene mupeza k*ti onse amene amakana za mtundu uwu kumakhala kuzikweza chabe km mitima yawo ikuvomeleza.
غايتنا إحياء التوحيد والسنة وإماتة الشرك والبدعة
kufikira ulendo wina tizafotokoze za mtundu wina in shaa Allah
kamng'ono kanu mchioembezo
Al-Qasweer Al salafiyy