13/07/2026
MATENDA A FOWL POX
Matenda Fowl Pox ndi amodzi mwa matenda omwe amasowetsa mtendere Kwa Alimi ambiri omwe amaweta nkhuku zambiri m'madera athu. Matendawa amayambitsidwa ndi kachilombo (virus) ndipo amakhudza kwambiri khungu la nkhuku limene lilibe Mapiko
Lero tiyeni tikambirane momwe tingazindikire matendawa, momwe amafakira, ndiponso njira zodzitetezera pogwiritsa ntchito njira zamakono komanso zachilengedwe.
☑️. ZIZINDIKIRO ZA FOWL POX
Zizindikiro zazikulu zimawonekera pankhope ndi mbali zopanda nthenga za nkhuku:
✅Ziphuphu kapena zilonda zakuda: Zimalowa m'maso, pamilomo, ndiponso pamiyendo.
✅Kutupa maso: Nthawi zambiri maso a nkhuku amatsekeka ndipo imalephera kudya chifukwa siona bwino.
✅Ulesisindi kufooka:Nkhuku zimangokhala monyong'onyeka ndipo zimataya mtima wodya.
*✅Kuvutika kupuma:Ngati kachilomboka kalowa mkamwa kapena pakholingo (wet pox), nkhuku imapuma movutikira ndipo imatha kufa msanga.
☑️2. Kodi Matendawa Amafala Bwanji
✅Udzudzu:Uyu ndi mdani wamkulu! Udzudzu ukaluma nkhuku yodwala, umapatsira nkhuku yathanzi ukadzailuma.
✅Kukhudzana: Nkhuku zathanzi zikagundana kapena kudya mbale imodzi ndi zodwala.
*✅Fumbi ndi Zida zodwalira:Kachilomboka kamatha kukhala m'fumbi la m'khola kwa nthawi yaitali.
---
☑️Njira Zopewera ndi Kulimbana ndi FOWL POX
Popeza matendawa amayambitsidwa ndi kachilombo (virus), alibe mankhwala enicho owathetsa nkhuku ikadwala kale.Choncho, njira yabwino kwambiri ndi kupewa
✅A. Katemera (Vaccination)
Uwu ndi mtetezi wodalirika kwambiri. Pelekani katemera wa FOWL POX kunkhuku zanu katemera wa Fowl Pox zikakhala ndi masabata 8 mpaka 10 (kapena malinga ndi malangizo a katswiri wa pafupi nanu).
B✅. Ukhondo ndi Kulimbana ndi Udzudzu
☑️ Chotsani madzi oyimirira pafupi ndi makola kuti muchepetse udzudzu.
☑️Thilani mankhwala oletsa tizilombo tomwe timayamwa magazi m'khola.
✅ C. Mankhwala a Zachilengedwe (Thandizo la Pakhomo)
Ngati nkhuku zanu zadwala kale, m***a kuzithandiza m'njira izi kuti zisamafe ndi njala kapena zofooka:
✅Kutsuka maso ndi zilonda:Sambitsani m'maso mwa nkhuku zodwalazo pogwiritsa ntchito madzi ofunda osakaniza ndi mchere pang'ono kuti zilonda zifewe ndipo maso atseguke kuti zizidya.
✅Kupaka Mafuta: Pakani zilondazo mafuta a Vaseline kapena mafuta ophikira osakaniza ndi khala kapena phulusa losalala kwambiri kuti zilondazo ziume msanga ndipo udzudzu usapitirize kuziluma.
✅Khonje kapena (Aloe Vera): Sakanizani madzi a khonje kapena Aloe Vera m'madzi akumwa a nkhuku zanu. Izi zimathandiza kulimbitsa chitetezo cha m'thupi la nkhuku kuti lilimbane ndi kachilomboko.
---
⚠️Uthenga kwa oweta onse:Matenda a fowl pox sachedwa kufalira, choncho nkhuku ikangowonetsa zizindikiro, ichoyseni MOMWE muli mzizame kayike payo payokha (quarantine) mwachangu!
* *