06/12/2025
Tinada nkhawa kwambiri
Yesu Ali ndi zaka 12, Yosefe ankatengaso banja lake kupita ku Yerusalemu. Inali nthawi ya chikondwelero Cha pasika ndipo mabanja akuluakulu amayendera limodzi. Ankayenda ndi nyama zonyamula katundu ndipo anadutsa mnjira zomwe zinali ndi msipu wobiriwira m'mbali mwake. Aluyandikira mzinda wa Yerusalemu, womwe unali pamalo okwera, n'kutheka kuti ambiri anayamba kuimba masalimo a nyimbo zokwerera ku mzinda. ( Sal 120-134 ) Pa nthawi ya chikondwelerochi, mumzindawu munali piringupiringu. Chikondwelerocho chitatha, mabanja onse anayamba ulendo wobwerera kwawo. Mwina chifukwa chotanganidwa, Yosefe ndi Mariya ankaona Ngati Yesu Ani naye limodzi pa ulendowo ndipo akuyenda ndi achibale ena. Koma atayenda nmtunda wa tsiku lathunthu, anazindikira kuti Yesu wasowa. Luka 2:41-44.
Nthawi yomweyi anayambaso ulendo wobwerera ku Yerusalemu ndipo anafufuza mmalo onse amene anadutsa. Taganizirani mmene mzindawo unkaonekera pa nthawiyi, anthu onse atapita, pamene Iwo ankayenda kwinaku akuitana Yesu. Kodi iye anali Ali kuti? Atafufuza kwa masiku atatu, mwina Yosefe anayamba kuda nkhawa kuti walephera udindo wake umene Yehova anamupatsa. Kenako anapita kukafufuza mkachisi. Iwo anafufuza paliponse mpaka anafika mchipinda chimene munali aphunzitsi odziwa bwino chilamulo ndipo mmenemo ndi mmene anampeza Yesu. Apa zoonekeratu kuti mtima wa Yosefe ndi Mariya umakhala Malo. Luka 2:45,46.
Yesu ankambetsetsa zimene aphunzitsiwo anakanena ndiponso ankawafunsa mafunso. Aphunzitsiwo anachita chidwi kwambiri ndi nzeru za mwanayo komanso mayankho amene ankapereka. Koma Mariya ndi Yosefe anadabwa kumpeza Ali kumeneko. Baibulo limasonyeza kuti Yosefe sanalankhure kanthu. Koma mawu amene Mariya analankhula akasonyeza maganizo amene makolo onsewo anali nawo. Iye anati: " mwanawe, m'chifukwa chiyani wativutitsa chonchi ? Ine ndi bambo Akowa tinada nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna." Luka 2:47,48.
Si ntchito yamasewera, ngakhare mwanayo atakhala wangwiro. Zimene zikuchitika m'dzikoli masiku ano zikuchititsa kuti kulera ana kuzipangitsa makolo kukhala ndi 'nkhawa kwambiri. ' komabe Iwo ayenera kudziwa kuti Baibulo limasonyeza mavuto amene akukumana nawo.
N'zosasangalatsa kuti Yesu anali pamalo amene ankaona kuti amuthandiza kuyandikira kwambiri kwa atate wake wakumwamba, Yehova. Iye anali ofunitsitsa kuphunzira zambiri za atate wake. Mchifukwa chake anayankha Malo ake kuti : " mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kupezeka mnyumba ya atate wanga ? Luka 2:49.
Yosefe ayenera kuti anaganizira mawu amenewa kambirmbiri mawuwa ankanyadira popeza anali atayesetsa kumuphunzitsa mwanayu kuti aziona kuti Yehova Mulungu ndi atate wake. Ngakhare kuti Yesu anali adakali mwana, ankakonda kwambiri Yehova ndipo
Ankamuona kuti ndi atate wake. Iye anakhala ndi maganizo amenewa chifukwa Cha zimene Yosefe ankaphunzitsa.
Ngati ndinu bambo, Kodi mumazindikira udindo umene muli nawo wothandizira ana anu kuti aziona kuti Yehova ndi atate wachikondi komanso amateteza anthu ake ? Nchimodzimodziso munalera ana oti si anu. Muyenera kutengera chitsanzo Cha Yosefe ndipo muziona kuti mwana aliyense ndi ofunika athandizeni kuyandikira kwa Atate wawo wakumwamba Yehova Mulungu. Aefeso 6:4.