Al-Da'watul Salafiyah Malawi

Al-Da'watul Salafiyah Malawi "The Quran and Sunnah according to the Understanding of the Pious Predecessors"

KODI MA SUFI AMAMUKONDADI MTUMIKI WA ALLAH ﷺ?!Mtumiki ﷺ adaletsa kukweza manda. Iwo adawakweza! Mtumiki ﷺ adaletsa kuman...
26/08/2026

KODI MA SUFI AMAMUKONDADI MTUMIKI WA ALLAH ﷺ?!

Mtumiki ﷺ adaletsa kukweza manda. Iwo adawakweza!

Mtumiki ﷺ adaletsa kumanga chiliza . Iwo adawakira manda !

Mtumiki ﷺ adaletsa kulemba pa manda. Iwo adawakongoletsa mkulembapo !

Mtumiki ﷺ adaletsa kupemphere kumanda. Iwo adapemphera ndi kuzungulira kumanda !

Mtumiki ﷺ adaletsa kupanga mzikiti pa manda kapena manda m'mzikiti. Iwo adayipanga kukhala mizikiti yofunika kwambiri yomwe ili ndi mamda mkati mwake !

Mtumiki ﷺ adaletsa kuwapanga manda kupita ngati zisangalalalo, koma iwo amapita kumanda pazisangalalalo zawo!

Mtumiki ﷺ adaletsa kuyenda ulendo wautali kupatula ku mizikiti 3. Iwo akuyenda ma ulendo a malo ochuluka kwambiri !

Mtumiki ﷺ adaletsa kupempha wina osakhala Allah. Iwo akupempha akufa ndi kuwapempha chitetezo!

Mtumiki ﷺ adaletsa kupembedza mafano ndipo adalamula kuwagumula. Iwo adawamanganso mwa masitayelo amakono!

Mtumiki ﷺ adaletsa kumvera zida zoimba/nyimbo. Iwo akuziyandikitsa kwa Allah ndi kumvera ndi kuvina pa nyimbo zoterozo!

Mtumiki ﷺ adaletsa kubweretsa zinthu zatsopano mu chipembedzo ndipo adati:
"Bid'a iliyonse ndi kusochera".
Iwo anamunamizira Allah ndi Mtumiki wake ndipo adati:
"Sikuti bid'a iliyonse ndi kusochera"!

Ndiye ndi Mtumiki uti amene mukunena kuti mukumukondayu?!

Wallahi ayi.Chisilamu sichipembedzo choseweretsa.Allah anati: "Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu". [Al-Maa'idah...
25/08/2026

Wallahi ayi.

Chisilamu sichipembedzo choseweretsa.
Allah anati: "Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu". [Al-Maa'idah: 3].
Ndipo Mtumiki ﷺ anati: "Amene abweretsa m'chipembedzo chathu chinthu chomwe sichiri mmenemo, chizabwenzedwa kwa iye". [Bukhari][Muslim]

Kodi izi ndizomwe Mtumiki ﷺ ndi Maswahaaba ankachita?
Ayi, sanazichite.

Mtumiki ﷺ ndi Maswahaba ankapembedza Allah potsatira Qur'an, Swalaah, Zikri wopanda kuvina, kuphunzitsa anthu, Jihad, kupereka sadaka, ndi kutsata Sunnah.

Zinthu monga kuvina, kulira ndi phokoso, kuvina ndi mwendo umodzi, kugwadira anthu, ndi "misonkhano ya ya Milad" - izi sizipezeka mu Sunnah ya Mtumiki ﷺ kapena mu ntchito ya Maswahaba .

Chifukwa chake akatswiri ambiri anena kuti zinthu izi ndi zatsopano mu chipembedzo, ndipo bidi'a iliyonse ndi kusochera.

Allah atitsogolere ku chowonadi ndi kutipangitsa kutsata Sunnah.
Follow our channel https://whatsapp.com/channel/0029VbAuO2L6GcGHCDgXLG46

Kodi pali kusiyana kotani pakati pa chipembedzo cha ma Sufi ndi chipembedzo chama hindu?Makamaka pachithunzi ichi palibe...
24/08/2026

Kodi pali kusiyana kotani pakati pa chipembedzo cha ma Sufi ndi chipembedzo chama hindu?
Makamaka pa
chithunzi ichi palibe kusiyana.

Kugwadira wina osati Allah (kaya ndi munthu kapena nyama) ndi shirk yaikulu yomwe imasemphana ndi chiyambi cha Tawhíd, chifukwa kupanga Sajdah ndi ibadah yompangira Allah yekha ndipo sikuloledwa kumpangira wina osakhala Allah.

Umboni wa ma Hadith:
"Ndikanakhala kuti ndikulamula munthu kugwadira munthu wina ndikanawalamula akazi kugwadira amuna awo". [Abu Dawud]

Kutanthauzira:
Kuletsa kugwadira cholengedwa chilichonse, ndipo kutsimikizira kuti ndi Allah yekha oyenera kupembedzedwa.

"E Allah musapange manda anga kukhala fano lopembedzedwa."[Ahmad]

Kuletsa kotheratu kupsola malire pa anthu kapena kuwapanga kukhala milungu yomwe imapembedzedwa posakhala Allah.

Follow our channel https://whatsapp.com/channel/0029VbAuO2L6GcGHCDgXLG46

Munthu kuti utumikire bwino Deen zimafunika ukhale ndi chochita chako choziimira pa wekha.Koma ukangokhala odalira ena m...
23/08/2026

Munthu kuti utumikire bwino Deen zimafunika ukhale ndi chochita chako choziimira pa wekha.

Koma ukangokhala odalira ena mavuto ake ndiawa omatenge hadith yokamba zakupeleka ndikumati ndiyololeza bidi'a.

Mtumiki ﷺ anati:
“Amene ayambitsa mu Chisilamu Sunnah yabwino, adzakhala ndi malipiro ake komanso malipiro a onse amene adzachite Sunnah imeneyo pambuyo pake, popanda kuchepetsedwa chilichonse pa malipiro awo.”
[Muslim 1017]

Nkhaniyi inachitika motere:
Tsiku lina anthu ena anabwera kwa Mtumiki ﷺ ali a njala ndi umphawi waukulu. Anali atavala zovala zong'ambika zopangidwa ndi ubweya.
Mtumiki ﷺ ataona mmene alili nkhope yake inaoneka ya chisoni.
Ndipo analimbikitsa Maswahaba kuti apereke sadaka.

Panthawiyo munthu wina wa Ansar anatenga chikwama chandalama n'kuchibweretsa. Kenako anthu ena anayamba kutsatira, wina ndi chakudya, wina ndi zovala, mpaka padasonkhana zinthu zambiri.

Pamenepo nkhope ya Mtumiki ﷺ inasangalala ndipo anati mawu awa:
“Amene ayambitsa mu Chisilamu Sunnah yabwino...”

Zofunika kumvetsetsa mawu akuti “سُنَّةً حَسَنَةً - Sunnah yabwino”:
Apa sizikutanthauza kupanga ibada yatsopano imene Mtumiki ﷺ sanaphunzitse.
Ayi. Amatanthauza kuzutsa chinthu chabwino chomwe chidalipo kale mu Chisilamu, monga kupereka sadaka, kuphunzitsa anthu, kumanga sukulu, kuthandiza anthu.

Mwachidule: Hadith iyi ndi yolimbikitsa kuchita zabwino ndi kutsogolera anthu ku chabwino, osati kupanga bidi'a mu chipembedzo.

Makani ena amakhala olumikizana ndi umphawi

Follow this link https://whatsapp.com/channel/0029VbAuO2L6GcGHCDgXLG46

⭕️ FUNSOKodi Allah anatilamula  ife kuchita izi ndi kukumbukira mtumiki wa Allah ndi machitidwe ndi kuvina ndi mwendo um...
23/08/2026

⭕️ FUNSO
Kodi Allah anatilamula ife kuchita izi ndi kukumbukira mtumiki wa Allah ndi machitidwe ndi kuvina ndi mwendo umodzi?
Kodi Mtumiki ﷺ kapena Maswahaaba adachita izi?

Machitidwe awa sanachokere kwa Mtumiki ﷺ ndipo sanachokere kwa Maswahaaba ake.

Follow Al-da'watul Salafiyah Malawi https://whatsapp.com/channel/0029VbAuO2L6GcGHCDgXLG46

|[ Chiyambi cha Maulidi a Mtumiki ﷺ ]|"Kukondwerera kubadwa kwa Mtumiki ﷺ ndi koletsedwa chifukwa cha maumboni akulu aku...
22/08/2026

|[ Chiyambi cha Maulidi a Mtumiki ﷺ ]|

"Kukondwerera kubadwa kwa Mtumiki ﷺ ndi koletsedwa chifukwa cha maumboni akulu akulu awa;

Woyamba: Kuti ntchito ya Maulidi ndi bidi'a yomwe sinachitike mu nthawi ya Maswahaba ndima tabi'eena, ndipo sikunachitike mmenemo kukondwerera kubadwa kwa Mtumiki ﷺ. Ndipo popeza zadziwika kuti ndi zatsopano ndiye ndi bid'a, ndipo bid'a iliyonse ndi kusochera monga momwe ma Hadith adatsimikizira kuchokera kwa Mtumiki ﷺ.

Umboni wachiwiri: Ndithudi Akatswiri amasiyana pa kudziwa tsiku la kubadwa kwa Mtumiki ﷺ m'mawu angapo:

➊ Ena adanena kuti ndi tsiku la 8 la Rabi'ul Awwal.
➋ Ena adati: Ayi, koma pa 10.
➌ Ena adati: Ayi, adabadwa pa 12.
➍ Ena adati: Ayi, adabadwa tsiku la 18.
➎ Ena adanena kuti Mtumiki ﷺ sanabadwe mu Rabi'ul Awwal ayi; adabadwa mu Rajab.

Kusiyana kwawo pa kudziwa kubadwa kwa Mtumiki ﷺ kumapangitsa kuti zisakhale zolondola za tsiku la 12 kuti pakondwerera kubadwa kwa Mtumiki ﷺ; chifukwa Akatswiri sanagwirizane za kubadwa kwake ﷺ pa tsikulo. Mwini wake wa ku Irbil adayesa kuthetsa vutoli, ndiye amakondwerera chaka chimodzi pa tsiku la 8, ndipo chaka china pa tsiku la 12, koma mawu a Akatswiri pa tsiku la kubadwa kwa Mtumiki ﷺ ndi ochuluka kuposa awa. Choncho akanayenera kuchulukitsa kukondwerera monga kuchuluka kwa mawuwo. Ndipo ichi ndi chinthu chabodza palibe kukayika;
chifukwa chotsimikizika ndi chakuti Mtumiki ﷺ kubadwa kwake sikunatsindikizike; adabadwa ﷺ tsiku limodzi lomwe ndi 8,10 ,12 malinga ndi mawu omwe atchulidwa kwa Akatswiri pa kusakhazikitsa tsiku la kubadwa kwa Mtumiki ﷺ.

Umboni wachitatu:Mwa zomwe Akatswiri adagwirizana ndi chakuti imfa ya Mtumiki ﷺ inali tsiku la 12 la Rabi'ul Awwal. Choncho ngati titavomereza kupanga tsiku limodzi, likanakhala kuti tsiku la chisoni pa Mtumiki ﷺ ndiloyenera kuposa tsiku la chisangalalo;
chifukwa tsiku lomwe Mtumiki ﷺ adabadwa silidziwika ndipo pali kusephana kwakukulu, koma tsiku lomwe Mtumiki ﷺ adamwalira adatsimikizira kuti ndi 12 Rabi'ul awwal...

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Al-Da'watul Salafiyah Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share