18/08/2026
UTHENGA WOTHOKOZA
Kwa semesita ino, ndili ndi chikhulupiriro chakuti tonse tidalitsidwa kwambiri ndi Joint Service. Choncho, ndikufuna kupereka ulemu ndi kuthokoza kwambiri kwa RELIGIOUS PRESIDENT, Mr. Benjamin Custom, chifukwa cha utsogoleri wake komanso khama lake pothandiza kuti ma service athu aziyenda bwino.
Komanso, ndikufuna kuthokoza kwambiri abusa athu amene anatsogolera service. Iwo ndi amene anatumikira ndi kutipatsa mawu a Mulungu omwe anatikhudza ndi kutilimbikitsa kwambiri. Zoonadi, maulaliki awo anali odabwitsa ndipo tatengapo madalitso ambiri.
Sitingathe kutchula aliyense payekhapayekha, koma kwa nonse amene munapezeka pa ma service komanso munathandizira m’njira zosiyanasiyana, tikunena kuti zikomo kwambiri. Kupezeka kwanu ndi kutenga nawo mbali kwanu kunathandiza kwambiri kuti Joint Service iyi ikhale yopambana.
Zikomo kwambiri nonse. Mulungu akudalitseni, akusungeni, ndipo apitirize kutitsogolera m’njira yake. 🙏❤️