Chinamwali private secondary schools

Chinamwali private secondary schools

Comments

2017 at Chinamwali private secondary schools in Zomba ,,pa nthawi imeneyo tili ma handsome 😂😂 ,6 yrs down the line... Ife tinkaphunzira Boyz yokhayokha.
Hi my daughter is schooling there so in need your help to discuss some issues
Ndizithu ziti zomwe uyenela kutenga pobwera ku school ko.. Ndafusa izi coz palimaschool ena ukamapita umatenga matress ndizina zotero ndeno unuso mumapanga chimoz moz ?
Remember munthu wina
Places are still available in all forms.

Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Chinamwali private secondary schools, School, Zomba.

Operating as usual

08/05/2023

Anzathu a private secondary, nkutheka simunapeze nawo mwai wolembetsa ma cluster komanso District mock, tatipezani pa 0997632929

Akonzekeretseni ana mokwanira bwino.

06/05/2023

Makhonzedwe aana.

Kwa dzaka zingapo tsopano, Zomba urban yakhala ikuchita bwino pokhonzetsa ana mayeso. Ndiife onyadira kuti tili sukulu imodzi imene ikupanga zapamwamba pa nkhani yokhonzetsa mayeso.
Ana akumakhonza ambiri kuyambira JCE komanso MSCE. Moti tikumapotsa masukulo aboma ochuluka ngakhale kuti ife pa sukulu yathu sitilandirapo ana ochita kusankhidwa. Kuno ana athu timatsula tonkha osatinso kungolandira oti anali kale mmasukulu aboma okupsya ipsya basi akakhonza mkumasokosa.
Timakhala ndi okhonza ochuluka komaso akhonza mwa quality.
Ma sukulu ambiri a private amapanga chinyengo chokuti amatha kupeza mwana wamzeru kwinakwake mkungomupatsa scholarship. Akangokhonza iyeyo iwo amasokosa ngati kuti akhonza ndi ana onse. Koma mukafufuza, ana ambiri amakhala atalephera mayeso. Kuno ife sitipanga chinyengo chitero. Aphunzitsi athu ndi odalilika omwe ali mkuthekera kotsula anawo mkuwapatsa tsogolo la bwino.

06/05/2023

School fees

Sukulu fees zathu nzotsika tikayerekezera ndi zimene zikuperekedwa kwinako.
Oyendera amapereka K85, 000 koma ogonera amapereka K290.00. Fees timalipira kawiri kudzera ku standard bank. Kuno timangofunako ma deposit slip basi.
Timalora kulipiranso kudzera njira za phone.
Cholinga chathu sikupanga ndalama. Tinayamba nkale sukuluyi, 1994 sipano. Ina ndi nthawi yothandizana ndi comunity, kwambiri ana ovutika.

Oachifukwachi, timaperekanso ma scholarship kwa oyendera komanso ogonera.

06/05/2023

Sukulu yathu ili ndi ubale wabwino ndi ma university odziwika mmalawi muno kotero ana ambiri ofuna kupanga ma teaching practice amawatumiza kuno komanso nafe timaba nzeru zochitira zinthu kudzera kwa akatakwe ophunzitsa kumeneko kudzera mma in service training omwe timapanga.
Kuno training timaiona kukhala yofunika kwambiri chifukwa knowledge siikhala static. Mu private zambiri, na Director amaona kuluza kumpatsa munthu training pomaganiza kuti achoka. Koma ife timadziwa kuti pa nthawi imene tikhale naye munthuyo tipindula koposa.
Training yangokhala ngati culture yathu.

06/05/2023

Mmene timachitira mmagwiridwe antchito..

Kuno timaonetsetsa kuti ndondomeko zimene unduna unakhazikitsa( ma standards) zikutsatidwa. Izi zimachitira ubwino ife komanso ana. Mzopindulitsa. Mwa chitsanzo, sitilora kuphunxitsa opanda scheme, lesson plan yoti yaonedwa kale. Timaonetsetsanso kuti ngati mphunzitsi akutsalira pa coverage ya ma topic, apeze njira amalizitse. Ana asamalembe mayeso asanamalize sylabus nkupanganso ma revisions. Munthu okanika kumaliza sylabus munthawi yake ngati palibe zotsamwitsa ndekuti alibe experience komanso ngwa ulesi .
Ntchito iliyonse imayenera kukhala ndi ma targets ndipo imayenera kuyezedwa. Kuno timakhala ndi performance apprisal kawiri pa chaka. Zotsatira zimatipatsa mwai oona mavuto ndipo zimapereka basis ya ma CPDs athu. Sitimangozuka mkumapereka ma training omwe sakuyankha mavuto athu.
Timakhulupiliranso kufunsana nzeru. Palibe amadziwa zonse. Munthu amatha kudziwa zinthu zina kwambiri koma mkukhala osadziwa kwambiri zinthu zinanso.
Timapanga supervision ya ma lessons pafupi pafupi. Timaonetsetsa kuti zomwe akulemba aphunzitsi zikugwirizana nzomwe akuphunzitsa komanso kuona ngati njira zophunzitsira zili zoyenerera.
Timalimbikitsa ma study circle.
Mayeso timalembetsa pafupipafupi.
Timakhala ndi makalasi apadera othandiza ana okumva movutikirapo.
Maphunziro a science kuno ana amakhonza mosavuta. Tilindi upangira osefukira kwambiri.

06/05/2023

Nkhani ya mwambo..(Discipline)

Kuno timakhulupilira mwambo. Mwana wasukulu azimvera malamulo. Mwana opanda mwambo kawiri kawiri sakhonza mayeso.
Timaonetsetsa kuti akutsata malamulo ndipo ngati aphwanyidwa malamulo amayenera kugwira ntchito mosaona nkhope. Kuno sitinyengerera mwana akamapanga zopusa. Timachotsa sukulu. Sitimalora mwana azisowetsa amzake mtendere chifukwa adalipira fees. Timangotenga fees yo mkumupatsa kuti akayambe kwina.
Timayesesa kulimbikitsa mwambo pogwirana manja ndi makolo. Sitipanga zinthu mwaife tokha.

06/05/2023

Tikupitiliza kufotokoza za sukulu yathu yomwe ili nayo mbiri yabwino.

Kuno timalandira mwana wina aliyese bola akhale ndi pass komanso sitilembetsa mayeso a entrance. Timakhulupilira kuti mwana aliyense ali ndikuthekera kochita bwino ngati wakumana ndi mphunzitsi oziwa ntchito yake. Kuno timaphika tokha osati kungomalizitsa zokupsya ipsya.
Aliyese alinako kuthekera.
Aphunzitsi omwe timalemba kuno kwambiri ndi omwe anali ku college za boma ndipo anakhonza bwino. Timaunikanso umunthu chifukwa munthu atha kukhala odziwa zinthu koma kamba kokula mtima, kusafuna kuphira kwa ena komanso kugwira ntchito ngati team, atha kusokoneza masomphenya.
Timakhulupilira kuti kulemba mphunzitsi yemwe anaphunzitsidwa bwino, odziwa ntchito pa ground, yemwe ali ndi self drive komanso passion ya ntchito apo zonse zimayenda mosavuta. Timakhilupilira gender equality. Komano sitingolemba poti uyu ndi mkazi kapena mamuna kutengera chisoni. Timalemba potengera competence.
Aphunzitsi athu ambiri amachonga nawo mayeso aboma choncho amazindikira zoyenera kuti mwana azichita bwino.
Mwachidule, Aphunzitsi athu onse kupatula m'modzi, ndi degree in education kuchokera ku chancellor college, Mzuzu university ndi Luanar basi.
Timalemba aphunzitsi munjira ya interview basi. Timakaona luso lawo popanga deliver lesson komanso pa oral, zaka zomwe aphunzitsako, sukulu zomwe aphunzitsako komanso ma results.
Timafuna kwambira azaka zapakati za 30 kupita mtsogolo, maturity komanso experience ndiyofunika.
Tinaika ndondomeko yakuti aphunzitsi omwe azikhonzetsa bwino azigulidwa ma grades awo.

05/05/2023

Mbiri ya Chinamwali pvt sec school mwachidule.

Sukuluyi inayamba mu chaka cha 1994. Mukumbuka bwino kuti pa nthawiyi titangolandira kumene ufulu wokhala ndi zipani zambiri. Chinamwali, inali sukulu imodzi mwa sukulu zochepa za pvt pa nthawiyo. Kungoyambira pomwe inayamba kupereka maphunziro, sukuluyi imatulutsa zotsatira za pa mwamba. Pachifukwachi, iyo yapititsa ana ochuluka zedi ku university ya Malawi kwa zaka zochuluka.
Lero mpovuta kupeza office kaya kampani imene ma bwana ake sanapondeko pa sukuluyi.
Pakupita pa nthawi, zinthu zinatipulumukako pang'ono moti zotsatira zathu zinayamba kusintha ndithu. Tadutsa munyengo yovutirapo pakatipa ndithu. Ambiri mwina amadabwanso kuti koma chinachitika ndi chiyani? Nkhani yaikulu ndi ma utsogoleri omwe tinali nawo muzaka za pitazi. Kuyambira pakalembedwe ka aphunzitsi, pa kayang'aniridwe ka ogwira ntchito komanso ana, zimativuta ndithu. Zotsatira zinthu zinatipulumuka ndithu.
Koma sitinatayebe chikhulupiliro ndipo tinayesesabe kukonza zina ndi zina kuti tidzukenso. Ndipo pa zaka ziwiri zapitazi tayesesa kuika m'malo ndondomeko zabwino kuonetsetsa kuti tiyendetse sukuluyi mwa ukadaulo ndipo tibwerere pomwe tinali. Zotsatira zayamba kuoneka sopano ndipo tsogolo likuoneka lowala ndithu.

Kodi tinachita chiyani kuti tikhalenso ndi sukulu yabwino?
√ Tinaunika za mavuto omwe tili nawo, mphamvu zathu, ziopsyezo komanso mwai omwe tili nawo okweza sukuluyi( SWOT analysis). Pamapeto pake tinabwera ndi plan yabwino yomwe tinapanga focus mbali zingapo motere;
1. Kulemba aphunzitsi a experience, okwanira m'maphunziro komanso a fungo la bwino pokhonzetsa ana. Sitilembanso aphunzitsi omwe luso lawo ndi lophunzitsa ku primary.
2. Tinalimbikitsa ma CPD's kuti aphunzitsi athu azikhala ndi luso, kuzikindira komanso upangiri wamakono wakagwiridwe ka ntchito. Timakhulupilira kuti nzeru zimalira kuzidyetsera.
3. Timalimbikitsa mwambo pa sukulu pathu kuyambira aphunzitsi kufikira ana. Kuno sitivomereza kujomba jomba, kupanga miss ma class chisawawa, kuchitira mwano aphunzitsi komanso kuthawa kuwerenga komanso kuthawa mayeso.
4. Timalembetsa mayeso apafupi pafupi komanso timakhala ndi maphunziro apadera othandiza ana ovutika kumva zinthu mwaulerere.
5. Aphunzitsi athu ngolimbikira ntchito kwambiri chifukwa amatenga uphunzitsi ngati maitanidwe.
6. Timalimbikitsa kulankhula chingerezi komanso ana athu timawalimbikitsa ma quiz omwe amapanga ndi sukulu zoziwika bwino pa malawi pano.
7. Timaonetsetsa kuti ma sylabus akumalizidwa nthawi yoyenera. Kuno timagwira ngati ku private sector komwe timafuna performance yabwino komanso ma results. Kulibe zongoti poti basi naipeza.
8. Tayesesa kupanga retain aziphunzitsi. Kunoko ndi private imene mphunzitsi amatha kufika ngakhale zaka 15 ndipo okhawo ogwira bwino ntchito, timawasunga ndithu chifukwa kuchotsachotsa aphunzitsi zimasokoneza ana.
9. Timakonda kuwaitanira ma role models ana athu kwambiri iwo omwe anapondako pa sukuluyi.
Mwachidule tinasintha machitidwe a business as usual. Tikutsimikizileni kuti sukulu yathu yabwerera mchimake ndipo ndi malo abwino oti m***a kutumiza ana anu. Tili ndi chikhulupiliro chonse kuti tichita bwino kwambiri pa mayeso aboma omwe atalembedwe chaka chino.

Malo alipo ambiri mmakalasi onse. Yimbani pa 0997632929

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 05/05/2023

MSCE MOCK IN PROGRESS

15/04/2023

We are re-branding and re-positioning. Be part of this exciting journey.

14/04/2023

ZIFUKWA ZINA ZOBWERETSERA ANA PA SUKULU YATHU.
* Timakhulupilira kukhala ndi mwambo kuyambira aphunzitsi, komanso ana asukulu. Mwambo ukasowa pa malo palibe chimayenda.

* Sitimangolembapo aphunzitsi mwachisawawa. Ngakhale akhale kuti analandira ukadaulo wa maphunzitsidwe, timayesesa kuwapanga interview kuti tione mmene akupangira deliver komanso kuona mbali ya u munthu wao.

* Timalimbikitsa maphunziro apadera kuti titumikire ana ovutika kutsatira zinthu mofulumira. Kotero, tikangoweruka pamakhala makalasi apadera ndithu kwambiri mma phunziro a science. ( Ana kuno amakhonza science kwambiri).
* Tili ndi diet yabwino zedi. Ndi school imodzi mwa zochepa zomwe ana amadya nkhukhu kawiri pa sabata komanso msima ya ufa wa Gramil.

* Tili ndi PTA yamphamvu yomwe imaonetsetsa kuti zinthu zikuyenda nchimake.

* Kuno munthu kuti akhalitse pa ntchito zimayendera perfomance sizongoti basi bola walowa ayi.

* Timaonetsa kuti ana azitha kuyankhula bwino chingerezi. Nchifukwa timalimbikitsa ma quiz mmasukulu oziwika bwino.

* Sukulu yathu ili pa malo osavuta kuwafikira.

* Kuno kulibe zolembetsa ma Entrance, chifukwa tilindi ukadaulo ophunzitsa ana anuwo mkuwasintha kuti azimva zomwe enawo zimawakanika kuchita. Mphunzitsi weni weni azitha kusintha vuto la mwana osangodalira okhao anzeru.

* Tili ndi Laboratory komanso library.

* Timalimbikitsa mapemphero kwambiri.

* Timalimbikitsa kuphunzitsa kotsata ndondomeko zokhadzikitsidwa ndi unduna wazamaphunziro.

* Kuno sitilemba aphunzitsi omwe anaphunzitsidwa kukaphunzitsa ku primary kapenanso omwe alibe degree komanso diploma. Timalemba kwambiri omwe anapita ku university za boma, omwe ali ndi experience yokwanira komanso okhwima nzeru.

* Tili ndi chitetezo champhavu .

* Timakhala ndi ana ochepa mmakalasi mwathu kuti tiziwatumikira moyenerera.

* Timalemekeza ufulu wa chibadwidwe wa anthu komanso wa chipembezo.

* Sukulu fees yathu ndiyosaboola nthumba.

* sukulu yathu ili ndi centre.

Imbani pa 0997632929 lero.

12/04/2023

Dokotala wabwino, oziwa ntchito yake, sakana odwala. Iye amaunika vuto la odwalayo mkumupatsa chithandizo choyenera.

Mkuthekatu muli ndi mwana yemwe akukukaikitsani ngati atakhonze mayeso a JCE komanso MSCE. Mwinanso mukaona nthawi yasalayi mukuona ngati nzosatheka kuti angazitorere mkukhonza.
Ife tili nawo ukadaulo otha kumutsegula mwanayo mutu mwakanthawi kochepa mkum***andizira kuti akhonze. Timalandira ana okuti anapangidwa w**d kwinako koma mkuwasula mokwanira mpaka mkupedza certificate. Kodi zimatheka bwanji?
Choyamba taphunzitsa zaka zochuluka mokuti sylabus ya MSCE timachita kuziwilatu kuti chaka chino ana tiwapange drill kwambiri mbali izi ndi izo ndipo amakumanadi nazo. Sizongophunzitsapo chisawawa.

Mwina timamphunzitsa kuti asangoloweza. Maphunziro monga science siovuta mmene wena amaonera komano nkhani ndiyakuti ophunzitsayo azimupanga mwana kuganiza osati kuloweza.

Timampatsa mwana ntchito pafupi pafupi kuti tione mmadera omwe akufunikaso thandizo asanalembe mayeso.
Kuno timaphunzitsa nthawi zapadera kuti tiwatikire anawo molingana mkuthekera kwao. Sizipophunzitsa ngati kuti ana onse amaganiza mofanana.
Njira za ife zophunzitsira zimampatsa mwanayo kachikoka koikonda subject. Osati kumangolondola bukhu mmene lilili ayi.
Zambiri muzamva mukambweretsa mwanayo.

Ife tikukupangani challenge kuti nthawi yatsalayi ndi yokwanira ndithu chifukwa ukadaulo wathu ndiokwanira kwambiri. Mphunzitsi weni weni amapanga zosathekazo kuti zitheke. Timakonda ana omwe sanasankhidwewo akapezeke ku university
limodzi anzawo osankhidwawo.

Call: 0997632929

12/04/2023

WE ARE REGISTERING STUDENTS FOR THE THIRD TERM.
Places are available in all forms.
0997632929.

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 04/04/2023

Dear Parents, Guardians and prospective students,

The just ended term has been very incredible! Our commitment at Chinamwali Private Secondary school, is to provide a safe and intellectually challenging environment that will empower students to become innovative thinkers, creative problem solvers and inspired to learn to thrive in the twenty first century.
High standards and expectations for each student in regard to academic performance, co-carricular participation,and responsible citizenship are the foundation of our SCHOOL. It is with pride that we hold these high standards and ask each of our students to commit to maintaining the extraordinary record of achievement and contribution, that has been the legacy of our students.
Below are our beliefs Regarding teaching and learning that we have developed to continue with our legacy.
We believe that effective teachers
:Create opportunities for intellectual development, collaboration,problem solving and applications of classroom learning in real life situation: implement strategies that promote ownership of learning of students, design instruction to integrate a variety of tech tools and resources to enhance learning: demonstrate ongoing professional growth in order to increase, the quality of instruction: collaborate with colleagues to share and discuss exemplary practices: interpret students performance data and design assessments that promotes twenty first century skills.
We believe that successful students:
Communicate in a meaningful way for a variety of purposes and audiences: Demonstrate a sensitivity to precision and Nuance of written,visual and oral medium through comprehension, interpretation, and evaluation: pose questions, examine
Possibilities and apply skills to find solutions to authentic issues: Make positive choices related to mental wellness and contribute to local and global community in a collaborative and respectful manner.
Wishing you all wonderful term. Places are still available.

Call : 0997632929 Today.

" Learning together, Achieving together. "

04/04/2023

Zinyambe kuiwalika.

QUIZ

Chinamwali pvt sec school students kuyesana mphamvu ndi St Marys girls secondary school.

Ana azitha kulankhula chingerezi

Tawatumizeni anawo kuno azalandire maphunziro apamwamba.

0997632929.

16/03/2023

Ma fees athu ali motere:
Oyendera ndi k85, 000

Ogonera ndi k290.000.

13/03/2023

Mkufuna munthu odziwa mathematics kwambiri yemwe akukhala within zomba town. Muimbe pa 0997632929.

11/03/2023

Tangotsala ndi mnthawi yochepa kwambiri kuti mayeso alembedwe. Kukonzekera bwino mayeso mkofunika kwambiri kuti muzachite bwino.

Bwerani ku chinamwali private secondary school pa mnthawi ya holiday ikubwerayi kuti muzasulidwe mokwanira.

Aphunzitsi athu ali ndi experience yochuluka pa subjects zomwe amaphunzitsa.

Mtumizeni wanuyo ndipo ngakhale atakhala okaikitsa, kunoko azakhonza.

Tiyankhuleni pa 0997632929

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 19/02/2023

Our girls...

15/02/2023

Any good mathematician within Zomba....

Let's talk.... Especially if you are jobless.

0997632929.

11/02/2023
07/02/2023

Thanks to all those who applied for the post of languages and science teacher respectively. We have since filled the vacancy.

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 07/02/2023

Tsogolo lowala.

"Learning together Achieving together"

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 07/02/2023

Chinamwali private secondary school

03/02/2023

VACANCY ANNOUNCEMENT @
CHINAMWALI PRIVATE SECONDARY SCHOOL, PRIVATE BAG 37, ZOMBA.

POSITION: TEACHER

We are urgently looking for a qualified and experienced teacher to teach the following subjects ;

CHICHEWA AND LIFE SKILLS.( JCE level)

Applicants should have the following ;

Atleast a three year accredited diploma in education or it's equivalent from a public institution of higher learning. A degree will be an asset.

Must have atleast two years of teaching experience.

Should possess high degree of integrity and be ready to abide by our code of conduct.

Should have strong passion for teaching and be of initiative.

Should be aged between 20-40 years.

The school offers a reasonable salary commensurate with one's qualifications and experience.

Those interested should forward their copies of CVs coupled with cover letters to the Headeacher, Chinamwali private secondary school, private bag 37, Zomba, through Whatsupp number ,0997632929.

Closing date for receiving applications is sutuday 06th February,2023.

Chinamwali private secondary school is an equal opportunity employer, therefore women are greatly encouraged to apply.

Online Job Vacancies in Malawi - 2023 Best Jobs in Malawi 01/02/2023

Online Job Vacancies in Malawi - 2023 Best Jobs in Malawi

VACANCY ANNOUNCEMENT @
CHINAMWALI PRIVATE SECONDARY SCHOOL, PRIVATE BAG 37, ZOMBA.

POSITION: TEACHER

Source: onlinejobmw.com

Typed By: Idu Mwawa
(0999 45 20 22 /0880 800 935)

MWAWA's NOTE:
1) Do Not Pay Money To Get a Job. Legitimate Employers will never ask you to pay Money to get a Job. Any person Charging a FEE for a Job is FRAUD.

2) Editing is NOT permitted BUT share as it is to all Job Vacancies Groups in order that our friends should try their Luck.

3) Are you looking for a Job in Malawi? Join Online Job Vacancies WhatsApp Group by sending "Add" to Mwawa's Inbox: 0999 45 20 22/0880 800 935.

4) To Access Job Vacancies from Online Job Vacancies WhatsApp Group is Free of Charge.

5) For More Job Vacancies and Other Adverts, Visit Our Website & Twitter:
Website: https://onlinejobmw.com/
Twitter: twitter.com/onlinejobmw

Close of Business: 04.02.23

POSITION: TEACHER

We are urgently looking for a qualified and experienced teacher to teach the following subjects:

Physics, Biology and Agriculture.

Applicants should have the following ;

•At least a three years accredited diploma in education or it's equivalent from a public institution of higher learning. A degree will be an asset.
•Must have atleast two years of teaching experience.
•Should possess high degree of integrity and be ready to abide by our code of conduct.
•Should have strong passion for teaching and be of initiative.

The successful candidate will also serve as the school's boarding master.

The school offers a reasonable salary commensurate with one's qualifications and experience.

MODE OF APPLICATION
Those interested should forward their copies of CVs coupled with cover letters to the Headeacher, Chinamwali Private Secondary School, Private Bag 37, Zomba, through WhatsApp number: 0997 632 929.

Interviews will be done on Saturday 4th February, 2023.

NOTE:
Search & Like Our page:
Online Job Vacancies
www.facebook.com/onlinejobmw

Copyright © 2023 ONLINE J

Online Job Vacancies in Malawi - 2023 Best Jobs in Malawi online Job vacancies in malawi is a platform that gives you latest jobs in Malawi, training adverts, and consultancy on time. your careers is here

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 29/01/2023

QUIZ TIME

Our students battling it out against students from St Mary's girls secondary school in Zomba, on Friday.

We lost narrowly by 46-40.

Our heart felt gratitude to the leadership and entire staff of St Mary's Girls secondary school For YOUR kind gesture.

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 29/01/2023

It was a marvel to watch. Chinamwali private secondary school again St Mary's girls secondary school.

"To be the best , learn from the best."

28/01/2023

Vacancy Announcement

Teacher ( sciences)

We are urgently looking for a teacher to teach the following subjects at JCE level;

Physics, Biology and Agriculture.

The ideal candidate should possess the following;

Atleast a diploma or degree in education from government accredited institution of higher learning.

Must have Atleast two years teaching experience( those who were on government internship program will have an added advantage)

Should be twenty-five years and above.

Those interested should forward their Cvs plus cover letters to us through the following whatsap number; 0997632929. All applications Should be addressed to the headtecher, Chinamwali private secondary school, private bag 37, Zomba.

To reach him not letter than Sunday, 29 January,2023.

Chinamwali private secondary school is an equal opportunity employer, therefore women are greatly encouraged to apply.

Photos from Chinamwali private secondary schools's post 19/01/2023

Kumvetsera mwatcheru ndondomeko zopewera cholera pa school kuchokera Kwa azaumoyo.

Wanuyo akhala otetezeka kuno.

04/01/2023

Bwerani muzapindule ndi maphunziro apamwamba nkuzasangalala ngati anzanuwa. Nzotheka ndithu.

Imbani pa 0997632929. Malo aliko ambiri makalasi onse.

30/12/2022

School zikuyamba pa 3
January pomwepa. Kodi mwapeza kale school yabwino komwe mungatumize ana anu?
Chinamwali private secondary school ndi school yakale kwambiri pa ma school a private mmalawi muno ndipo yatumiza ana ochuluka ku ma university komanso college za boma.
School ya chinamwali, ndi ya ana oyendera komanso ogonera, anyamata ndi atsikana.
School ya chinamwali ili ndi chitetezo chokwanira, hostels ochuluka, ma kalasi ambiri, ana amaphunzira ochepa pa kalasi iliyonse kuti azimvetsetsa komanso aphunzitsi satenga subjects zopitilira ziwiri ( ma periods sadutsa 18) kuti azitha kumaliza mofulimira syllabus komanso asakhale pa mpanipani.
Kuno sitilembetsa ma entrance chifukwa tili ndi aphunzitsi okutha kusula ana omwe kwinako akanidwa mkuwatembenudza kukhala nkuthekera. Ifetu tilingati chipatala. Sitikana odwala. Timamuyeza kupedza vuto lake mkumpatsa thandizo loyenerera.
Fees zathu mzosaboola mnthumba. K290.000 ogonera. K85.000 oyendera. Plus k5.000 registration fee.
Kunotu chakudya timapereka chabwino. Ndi sukulu imodzi mwa sukulu zochepa zomwe zimadyetsa ana nkhuku,komanso gramil. Kulibe za ngaiwa zoumira kuno.
Timamvetsetsa pa nkhani ya fees malinga ndi mavuto azachumawa.
Pa nkhani ya discipline sitisekerera. Timakhulupilira kuti mwambo ngofunika. Democracy posaimvetsa ikuononga maphunziro. Akamabwera mwanayo akonzeke kumvera malamulo, apo ayi azachotsedwa.
Kuno timayesesa kuphunzitsa mozipereka kuti gulu likhonze. Akalephera mwanayo ndekuti zinatikanika ndithu.
Timakhulupilranso kugwira ntchito ndiinu makolo omwe ndi ma strategic stakeholders pamaphunziro. Tili ndi P.T.A ya mphamvu.
Pa nkhani ya aphunzitsi ndiye tisaziimbire tokha lipenga. Tili ndi aphunzitsi a experience yabwino ena ophunzitsa mmboma komanso school zotchuka potulutsa ma results muno mmboma la zomba. Nzofunika mwana azithandidwa nda akatakwe kuti azathe kuchita bwino.
Imbani phone pa 0997632929 or mutipeza pa whatsup pa number yomweyi.

Kulibe zopereka commitment fee kuno.

23/12/2022

VACANCY ANNOUNCEMENT

We are looking for a teacher to teach a combination of MATHEMATICS and PHYSICS at MSCE level.

Qualification: Bachelor degree of Education( sciences) preferably from public university /college, with a minimum of 3 years teaching experience.

Those interested to work on part-time arrangement are also welcome so long they are currently teaching at the aforementioned level in their respective public secondary schools.

Those with a distinction in additional mathematics on their MSCE will have an added advantage.

Interested candidates are requested to send their up to date CVs plus cover letters, to the Headteacher, Chinamwali private secondary school, Private Bag 37, Zomba , through Whatsupp number 0997632929.

To reach him not later than 26 December,2022. Those who do not meet the above requirements should not apply.

Chinamwali private secondary school is an equal opportunity employer, therefore women are greatly encouraged to apply.

"Learning together,Achieving together."

23/12/2022

Choosing the right school and the right education system for your child might be the most important and also the most impactful decision of their future that shapes who they are. China's private secondary School might be the best decision you could take for your child.

Choose chinamwali private secondary school and you won't regret it.

Places are plenty in all forms.

Call or whatsap 0997632929.

"Leaning together,Achieving together."

22/12/2022

We are still registering students for the 2023- JCE and MSCE maneb examinations.

Register with us and you won't regret.

Call us today on 0997632929.

21/12/2022

Good news from chinamwali private secondary schools

scholarships....

Target group

Those who sat for the two previous MANEB examinations and managed to score an aggregate 20-30 points and would to lower their grades.

Conditions of scholarship
1) Prospective students should be prepared to pay their fees for the 2023 MANEB examinations
2) Required to pay half of school fees,
Boarding fees is currently at MK 290,000 and day is pegged at 85,000 so half of that.

Please Hurry and reconsider your future!!! Make Chinamwali Secondary school part of your stepping stone to your desired career...

It's now or never!!!

21/12/2022

Good news from chinamwali private secondary schools

scholarships....

Target group

Those who sat for the two previous MANEB examinations and managed to score an aggregate 20-30 points and would to lower their grades.

Conditions of scholarship
1) Prospective students should be prepared to pay their fees for the 2023 MANEB examinations
2) Required to pay half of school fees,
Boarding fees is currently at MK 290,000 and day is pegged at 85,000 so half of that.

Please Harry and reconsider your future!!! Make Chinamwali Secondary school part of your stepping stone to your desired career...

It's now or never!!!

21/12/2022

Good news from chinamwali private secondary schools

scholarships....

Target group

Those who sat for the two previous MANEB examinations and managed to score an aggregate 20-30 points and would to lower their grades.

Conditions of scholarship
1) Prospective students should be prepared to pay their fees for the 2023 MANEB examinations
2) Required to pay half of school fees,
Boarding fees is currently at MK 290,000 and day is pegged at 85,000 so half of that.

Please Harry and reconsider your future!!! Make Chinamwali Secondary school part of your stepping stone to your desired career...

It's now or never!!!

Call or whatsap 0997632929

18/12/2022

Kodi mwapanga kale chisankho cha sukuluku yomwe mutumizeko mwana wanu?
Tayesani kumtumiza mwanayo ku chinamwali private secondary school, ku zomba ndipo simuzakhumudwa.

Sukulu yathu imalimbikitsa kaphunzitsidwe kothandiza mwanayo kuti aziganiza osati kumangopatsidwa information ngati ulaliki wamutchalitchi.

Timaonetsetsanso kuti chidwi chamwanayo chikhale pa ma phunziropo kuposa china chilichonse. Ichi mchifukwa timalimbikitsa ma study circles, ma homework, ndizina kuti ana azikhala busy. Timakhalaso ndi ma phunziro apadera ongoonjezera mwaulere kwa ana omwe akuvutika kutsata msanga zinthu. Mukamabweretsa mwanayo ayembekezere kuphunzira ngakhale weekend.

Timachita zinthu zanthu mogwirizana ndi makolo chifukwa maganizo anu ndofunika kwambiri pa momwe sukulu iyenera kupita chitsogolo.

Timalimbikitsa mapemphero mwa anawa chifukwa muzonse timangoyenera kudalira ambuye basi. Kupanga ma plan mkaife koma okwaniritsa ndiye mwini.

Timakhulupilira kuti ana amaphunzira komanso kuchita bwino ngati ali ndi chikhulupiliro mwa aphunzitsi awo. Ichi mchifukwa timayesesa kupeza aphunzitsi abwino kwambiri pa subject iliyonse kuti ana azimvetsetsa kwambiri. Kuno potenga mphunzitsi timafuna kwambiri a education plus akhale nayo experience yambiri. Ndipo amayesedwa both oral and practical teaching.

Timalimbikitsa anawa kuwapatsa mayeso pafupipafupi kuti ziziwathandiza komanso amalemba mock zochuluka kuchoka ma clusters kuti akonzekere mokwanira.

Timalimbikitsa chikhalidwe chabwino. Ana osamvera malamulo timachotsa ndithu. Khalidwe nkukhonza zimayenderana. Sukulu za chikatolika zimachitanso kwambiri chifukwa sasewera pa nkhani ya discipline.

Timaonetsetsanso kuti ma syllabus akumalizidwa nthawi yoyenerera. Mzofunika izi chifukwa ana amachita bwino. Mwana sitingomphunzitsa kuti akhonze kokha mayeso koma asakavutike komwe akupitako.

Timatsata ndondomeko zonse za ministry pankhani za maphunziro ndipo tikuyesesabe kulimbikitsa izi koposa.

Fees zathu mzomvelerako poganizira mavuto

Want your school to be the top-listed School/college in Zomba?

Click here to claim your Sponsored Listing.

Videos (show all)

Listen to our Audio.

Location

Category

Telephone

Website

Address

Zomba
265
Other Schools in Zomba (show all)
Mubarak Complex College Mubarak Complex College
Mubarak Complex College, P. O Box 1058 Zomba
Zomba

RECOGNIZED & REGISTERED by the Malawi Government through TEVETA, located in Zomba township.

Drepar community day secondary school Drepar community day secondary school
Zomba

Located in Zomba district, in maluwa villagw close to bulaymana primary scholl

Essenberg Montessori School Essenberg Montessori School
Chinamwali , Habitant
Zomba

Essenberg montessori pre-school offers an individualised and safe learning Environment that responds

UTALE UTALE
Balaka
Zomba

Its all about utale secondary

cassim Islamic academy cassim Islamic academy
Zomba

A SCHOOL THAT GIVE ISLAMIC AND SECULAR EDUCATION

Lusolathu Private Secondary School. Lusolathu Private Secondary School.
Zomba

Lusolathu is situated at Malosa near Malosa CCAP sign post. The school offers quality education. It

The Little Scholars:Zomba The Little Scholars:Zomba
Zomba

The Little Scholars an institution that strives for cultural diversity.

Ulumba Community Day Secondary school Ulumba Community Day Secondary school
Lambulira
Zomba

Ulumba CDSS is situated in Zomba rural Lambulira side

Hi profile pvt secondary school Hi profile pvt secondary school
Zomba, 1190002356126535